Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamre, pamene anakhala pa khomo la hema wace pakutentha dzuwa. |
| 2 |
| Ndipo anatukula maso ace, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pace; pamene anaona iwo, anawathamangira kucoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati, |
| 3 |
| Mbuyanga, ngatitu ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu; |
| 4 |
| nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo; |
| 5 |
| ndipo ndidzatenga cakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, cifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Cita comweco monga momwe wanena. |
| 6 |
| Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wace kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate. |
| 7 |
| Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng'ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika. |
| 8 |
| Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng'ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pao; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya. |
| 9 |
| Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m'hemamo. |
| 10 |
| Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yace; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pace. |
| 11 |
| Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, ana pitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumacita ndi akazi; |
| 12 |
| ndipo Sara anaseka m'mtima mwace, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba? |
| 13 |
| Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba? |
| 14 |
| Kodi ciripo cinthu comlaka Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yace, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna. |
| 15 |
| Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; cifukwa anaopa, Ndipo anati, lai; koma unaseka. |
| 16 |
| Ndipo anthuwo anauka kucokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza. |
| 17 |
| Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu cimene ndicita? |
| 18 |
| Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkuru ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye? |
| 19 |
| Cifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ace ndi banja lace la pambuyo pace, kuti asunge njira ya Yehova, kucita cilungamo ndi ciweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu comwe anamnenera iye. |
| 20 |
| Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukuru, ndipo popeza kucimwa kwao kuli kulemera ndithu, |
| 21 |
| ndidzatsikatu ndikaone ngati anacita monse monga kulira kwace kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa. |
| 22 |
| Ndipo anthuwo anatembenuka nacoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova. |
| 23 |
| Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa? |
| 24 |
| Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowa cifukwa ca olungama makumi asanu ali momwemo? |
| 25 |
| Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzacita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi? |
| 26 |
| Ndipo anati Yehova, Ndikapeza m'Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi, ndidzasiya malo onse cifukwa ca iwo. |
| 27 |
| Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine pfumbi ndi phulusa: |
| 28 |
| kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mudzi wonse cifukwa ca kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga. |
| 29 |
| Ndipo ananenanso kwa iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi anai. |
| 30 |
| Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzacita. |
| 31 |
| Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi awiri. |
| 32 |
| Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwakhumim'menemo: Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca khumi. |
| 33 |
| Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwace. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/genesis/018.mp3
50
18