Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu: |
| 2 |
| Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi |
| 3 |
| ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti. |
| 4 |
| Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli; |
| 5 |
| ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani. |
| 6 |
| Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo. |
| 7 |
| Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi. |
| 8 |
| Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri. |
| 9 |
| Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri. |
| 10 |
| Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau: Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau. |
| 11 |
| Awa ndi mayina a ana a Elifazi: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi. |
| 12 |
| Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau. |
| 13 |
| Awa ndi ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau. |
| 14 |
| Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa: Yeusi, Yolamu ndi Kora. |
| 15 |
| Nawa mafumu a zidzukulu za Esau: Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa: Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi, |
| 16 |
| Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada. |
| 17 |
| Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau. |
| 18 |
| Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa: Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana. |
| 19 |
| Amenewa ndiwo zidzukulu za Esau (amene ndi Edomu) ndiponso mafumu awo. |
| 20 |
| Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, |
| 21 |
| Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori. |
| 22 |
| Ana aamuna a Lotani anali awa: Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani. |
| 23 |
| Ana aamuna a Sobala anali awa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. |
| 24 |
| Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni. |
| 25 |
| Ana a Ana anali: Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi. |
| 26 |
| Ana aamuna a Disoni anali awa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani. |
| 27 |
| Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Akani. |
| 28 |
| Ana aamuna a Disani anali awa: Uzi ndi Arani. |
| 29 |
| Mafumu a Ahori anali awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, |
| 30 |
| Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri. |
| 31 |
| Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko: |
| 32 |
| Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba. |
| 33 |
| Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake. |
| 34 |
| Atafa Yobabu, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa mʼmalo mwake ngati mfumu. |
| 35 |
| Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti. |
| 36 |
| Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka, analowa ufumu mʼmalo mwake. |
| 37 |
| Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje, analowa ufumu mʼmalo mwake. |
| 38 |
| Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake. |
| 39 |
| Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. |
| 40 |
| Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa: Timna, Aliva, Yeteti, |
| 41 |
| Oholibama, Ela, Pinoni, |
| 42 |
| Kenazi, Temani, Mibezari, |
| 43 |
| Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu molingana ndi malo awo okhala mʼdzikomo. Umenewu ndi mndandanda wa mʼbado wa Esau, kholo la Aedomu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/genesis/036.mp3
50
36