Mibadwo ya Yakobo ndi iyi: Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ace; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate wace; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wace mbiri yao yoipa.
Ndipo analotanso lata lina, nafotokozera abale ace, nati, Taonani, ndalotanso lata lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.
Ndipo iye anafotokozera atate wace ndi abale ace; ndipo atate wace anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amai ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi?
Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta ziri bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kucokera m'cigwa ca Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.
Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m'dzenjemo m'cipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye ra'manja mwao, ambwezenso kwa atate wace.
Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye cakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismayeli anacokera ku Gileadi ndi ngamila zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi libano alinkumuka kutsikira nazo ku Aigupto.
Ndipo ana pita pamenepo Amidyani a malonda: ndipo anamturutsa namkweza Yosefem'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismayeli ndi ndalama zasiliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Aigupto.
Ndipo ana amuna ace onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndirinkulirabe. Atate wace ndipo anamlirira.