|
| 1 |
|
| Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu. |
|
| 2 |
|
| Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.” |
|
| 3 |
|
| Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti. |
|
| 4 |
|
| Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
|
| 5 |
|
| Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira. |
|
| 6 |
|
| Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi. |
|
| 7 |
|
| Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
|
| 8 |
|
| Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira. |
|
| 9 |
|
| Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani. |
|
| 10 |
|
| Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
|
| 11 |
|
| Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira. |
|
| 12 |
|
| Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli. |
|
| 13 |
|
| Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
|
| 14 |
|
| Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira. |
|
| 15 |
|
| Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi. |
|
| 16 |
|
| Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
|
| 17 |
|
| Zaka zonse za Mahalaleli zinali 895 ndipo anamwalira. |
|
| 18 |
|
| Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki. |
|
| 19 |
|
| Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
|
| 20 |
|
| Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira. |
|
| 21 |
|
| Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela. |
|
| 22 |
|
| Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
|
| 23 |
|
| Zaka zonse za Enoki zinali 365. |
|
| 24 |
|
| Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga. |
|
| 25 |
|
| Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki. |
|
| 26 |
|
| Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
|
| 27 |
|
| Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira. |
|
| 28 |
|
| Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. |
|
| 29 |
|
| Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.” |
|
| 30 |
|
| Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. |
|
| 31 |
|
| Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira. |
|
| 32 |
|
| Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti. |
|
|
: |
| 1 | | 2 | | 3 | | 4 | | 5 | | 6 | | 7 | | 8 | | 9 | | 10 | | 11 | | 12 | | 13 | | 14 | | 15 | | 16 | | 17 | | 18 | | 19 | | 20 | | 21 | | 22 | | 23 | | 24 | | 25 | | 26 | | 27 | | 28 | | 29 | | 30 | | 31 | | 32 | 1
1
1 |
|
|---|
|
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/genesis/005.mp3
50
5