Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera. |
| 2 |
| Tsono akasupe a madzi ambiri a pansi pa dziko ndi zitseko za madzi a kumwamba zinatsekedwa, ndipo mvula inaleka kugwa. |
| 3 |
| Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika, |
| 4 |
| ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati. |
| 5 |
| Madzi anapitirira kuphwa mpaka mwezi wa khumi, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wa khumiwo msonga za mapiri zinayamba kuonekera. |
| 6 |
| Patapita masiku makumi anayi, Nowa anatsekula zenera limene anapanga mʼchombomo |
| 7 |
| natulutsa khwangwala, koma khwangwalayo ankangowuluka uku ndi uku mpaka madzi anawuma pa dziko lapansi. |
| 8 |
| Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko. |
| 9 |
| Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. |
| 10 |
| Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja. |
| 11 |
| Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi. |
| 12 |
| Iye anadikira masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatumizanso nkhunda ija, koma nthawi imeneyi sinabwererenso kwa iye. |
| 13 |
| Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. |
| 14 |
| Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu. |
| 15 |
| Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti, |
| 16 |
| “Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo. |
| 17 |
| Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.” |
| 18 |
| Nowa anatuluka pamodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake. |
| 19 |
| Nyama zonse, zokwawa zonse, mbalame zonse, chilichonse choyenda pa dziko lapansi, zinatuluka mʼchombo motsogozana monga mwa mitundu yawo. |
| 20 |
| Pamenepo Nowa anamanga guwa lansembe la Yehova ndipo anatengako mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya ndi mbalame zoti nʼkudya naperekapo nsembe yopsereza. |
| 21 |
| Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu. |
| 22 |
| “Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola yozizira ndi yotentha, dzinja ndi chilimwe, usana ndi usiku, sizidzatha.” |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/genesis/008.mp3
50
8