Choncho chikondwerero cha tsikulo chidasanduka maliro kwa anthu onse, pakuti anthu adamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake.
Tsono Yowabu adaloŵa m'nyumba ya mfumu nakafika kwa mfumu, nati, “Inu lero mwachititsa manyazi ankhondo anu amene apulumutsa moyo wanu, ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu,
Mfumu Davide adatumiza mau kwa ansembe aja, Zadoki ndi Abiyatara, akuti, “Mufunse atsogoleri a ku Yuda kuti, ‘Chifukwa chiyani inu mukuzengereza kwambiri osakaitenganso mfumu kuti ibwerere ku nyumba kwake, pamene Aisraele onse atumiza kale mau kwa mfumu onena kuti mfumu ibwerere kunyumba kwake?
Choncho Davide adakopa mitima ya Ayuda onse, ndipo adamangana chimodzi. Motero anthuwo adatumiza mau kwa mfumu kuti, “Bwererani inu pamodzi ndi ankhondo anu onse.”
Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a ku Benjamini. Zibanso mtumiki uja wa m'banja la Saulo, pamodzi ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndiponso antchito ake makumi aŵiri, adathamangira ku Yordani, nakafikako isanafike mfumu.
Koma iyeyo nkundisinjirira ine kapolo wanu kwa inu mbuyanga mfumu. Komatu inu muli ngati mngelo wa Mulungu. Nchifukwa chake tsono, muchite zimene zikukomereni.
Paja anthu onse a banja la bambo wanga anali oyenera kuphedwa ndi inu mbuyanga mfumu. Koma ine mtumiki wanu mudaandiika pakati pa anthu amene ankadya ndi inu pa tebulo lanu. Nanga ndingakhale ndi chiyaninso ine chimene chingandiyenereze kuti ndingadandaule kwa inu amfumu?”
Tsopano ine zaka zanga zakwana 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa zinthu zokondwetsa ndi zosakondwetsa? Kodi ine mtumiki wanu ndingathe kuzindikira kukoma kwake kwa zakudya kapena zakumwa? Kodi ine ndingathebe kumamvera kuimba kwa amuna ndi kwa akazi? Chifukwa chiyani ine mtumiki wanu ndikakhale ngati katundu wolemera wosanjikiza pa inu, mbuyanga mfumu?
Chonde, ingondilolani ine mtumiki wanu ndibwerere kuti ndikafere kumudzi kwathu, pafupi ndi manda a bambo wanga ndi a mai wanga. Koma suyu mwana wanga Kimuhamu, akhale mtumiki wanu. Iyeyu ndiye aoloke pamodzi ndi inu mbuyanga mfumu. Ndipo mumchitire chilichonse chimene chikukomereni.”
Mfumu idapitirira mpaka kukafika ku Giligala, ndipo Kimuhamu adapita nao. Anthu onse a ku Yuda ndiponso theka la anthu a ku Israele, onse adaperekeza mfumu.
Kenaka Aisraele onse adafika kwa mfumu, nadzafunsa kuti, “Chifukwa chiyani abale athu Ayuda achita ngati kukubani, nabwera ndi inu amfumu pamodzi ndi banja lanu ndi anthu anu onse, kuwoloka Yordani?”
Apo Aisraelewo adayankha Ayuda aja kuti, “Tili ndi zigawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo mwa ufumu wa Davide ife tili ndi zigawo zambiri kupambana inu. Nanga chifukwa chiyani tsono mukutinyoza? Kodi ife sindife amene tidayamba kulankhula zoti mfumu yathu ibwerenso?” Koma anthu a ku Yuda adalankhula mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israele.