Ndipo Yoabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwacurukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu acione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi cinthu ici?
Koma mau a mfumu anapambana Yoabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yoabu ndi atsogoleri a khamulo anaturuka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israyeli.
Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwoo Davide nati kwa Yehova, Ndinacimwa kwakukuru ndi cinthu cimene ndinacita; koma tsopano Yehova mucotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinacita kopusa ndithu.
Comweco Gadi anafika kwa Davide, namuuza, nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupitikitsani miyezi itatu? kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Cenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.
Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndacimwa ine, ndinacita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinacitanji? dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.
Arauna nati kwa Davide, Mbuye wanga mfumu atenge napereke nsembe comkomera; sizi ng'ombe za nsembe yopsereza, ndi zipangizo ndi zomangira ng'ombe zikhale nkhuni;
Koma mfumu inati kwa Arauna, lai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wace, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wace. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva.
Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka cifukwa ca dziko, ndi mliri wa pa Israyeli unalekeka.