Konse kumene ndakhala ndikuyenda ndi Aisraele onse, kodi ndidaauzapo ndi mmodzi yemwe mwa aweruzi a Aisraele, amene ndidaŵalamula kuti azisunga anthu anga, kuti, bwanji sudandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?
Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzakumveketsa dzina lako kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi.
Ndipo ndidzaŵasankhira malo anthu anga Aisraele, ndi kuŵakhazika kumeneko kuti akhale ku malo aoao popanda kuvutikanso. Anthu achiwawa sadzaŵazunzanso monga momwe adaachitira kale lija,
kuyambira nthaŵi imene ndidaaika aweruzi a anthu anga Aisraele. Choncho ndidakupumitsa kwa adani ako onse. Kuwonjezera pamenepo, Chauta akukuuza kuti, Ine Chauta ndidzakhazikitsa banja lako.
Masiku ako atatha kuti ulondole makolo ako ku manda, ndidzakuutsira chiphukira pambuyo pako, mmodzi mwa ana obereka iweyo, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kolimba.
Komabe zonsezi zinali zazing'ono kwa Inu Chauta Wamphamvuzonse. Mudalankhulanso za banja la ine mtumiki wanu, kulilosera za nthaŵi yaikulu yam'tsogolo. Mwandionetsa mibadwo yam'tsogolo, Inu Ambuye Chauta.
Kodi ndi mtundu uti pa dziko lapansi uli wofanafana ndi anthu anu Aisraele, amene Inu Mulungu mudaŵaombola ku Ejipito kuti akhale anthu anu? Mudatchuka kwambiri poŵachitira zinthu zazikulu ndi zoopsa, ndiponso popirikitsa mitundu ina ya anthu pamodzi ndi milungu yao, pamene ankafika anthu anu.
“Tsopano Inu, Chauta Mulungu, musunge mpaka muyaya lonjezo lanu limene mudaachita ponena za ine mtumiki wanu ndi za banja langa. Muchite monga momwe mudaanenera.
Choncho dzina lanu lidzalemekezedwa mpaka muyaya. Anthu azidzati, ‘Chauta Wamphamvuzonse ndi Mulungu wolamulira Aisraele.’ Tsono banja la ine Davide, mtumiki wanu, lidzakhazikika mpaka muyaya.
“Inu, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Aisraele, mwandiwululira ine mtumiki wanu kuti mudzakhazikitsa banja langa. Nchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kuti ndinene pemphero limeneli kwa inu.
Tsono ndikukupemphani kuti mudalitse mokondwa banja la ine mtumiki wanu, likhalebe pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti mwatero ndinu Ambuye Chauta, choncho banja la mtumiki wanune lidzadalitsidwadi mpaka muyaya.”