Pambuyo pake Solomoni adasonkhanitsa akuluakulu Aisraele, ndi atsogoleri onse a mafuko, akuluakulu a mabanja a Aisraele. Onsewo adasonkhana kwa mfumu Solomoni ku Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta, kulitulutsa m'Ziyoni, mzinda wa Davide.
Pamenepo mfumu Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la Aisraele amene adaasonkhana pamaso pake, ataima patsogolo pa Bokosi lachipanganolo, ankapereka nsembe za nkhosa ndi ng'ombe zosaŵerengeka.
Tsono ansembe adafika nalo ndi Bokosi lachipangano la Chauta ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana, naliika kunsi kwa mapiko a akerubi.
Mphikozo zinali zazitali kwambiri, kotero kuti nsonga zake zinkaonekera kukhalira ku malo opatulika, patsogolo pa malo opatulika kopambana a m'kati aja. Koma kukhalira kunja sizinkaonekera. Ndipo zili komweko mpaka pano.
Ndipo mfumuyo idati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene wachitadi ndi dzanja lake zimene adaalonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide bambo wanga.
Tsopano Chauta wachitadi zimene adaalonjeza zija. Pakuti ine ndi amene ndaloŵa ufumu m'malo mwa Davide bambo wanga, ndipo ndikulamulira Aisraele pa mpando wa bambo wanga, monga momwe Chauta adaalonjezera. Ndipo ndinedi amene ndamanga Nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele.
Tsono m'menemo ndalikonzera malo Bokosi lija, m'mene muli mau a chipangano cha Chauta chimene adachita ndi makolo athu, pamene adaŵatulutsa ku Ejipito.”
Tsono adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, palibe Mulungu wina wonga Inu, kumwamba kapena pa dziko lapansi. Mumasunga chipangano ndi kuwonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtimi wao wonse.
Tsono, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, mukumbukire zimene zija mudalonjeza Davide bambo wanga, mtumiki wanu, pamene mudati, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa dziko la Israele, malinga ana ako akamasamala mkhalidwe wao, ndi kumayenda pamaso panga anga monga momwe iweyo wayendera pamaso panga.’
Imvani pemphero lopemba la mtumiki wanu ndiponso la anthu anu Aisraele, pamene akupemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mukhululuke.
“Anthu anu Aisraele atagonjetsedwa ndi adani ao chifukwa chakuti adakuchimwirani, pambuyo pake nkubwerera kwa Inu ndi kutamanda dzina lanu, napemphera ndi kupemba kwa Inu m'Nyumba muno,
Tsono, chodandaula chake chingakhale chotani, wina aliyense mwa anthu anu Aisraele akapemphera mopemba, akuzindikira zovuta za mumtima mwake, natambalitsa manja choloza ku Nyumba ino,
Zoonadi anthu adzamva ndithu za dzina lanu lotchuka ndiponso za dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu. Iyeyo akabwera kudzapemphera ku Nyumba ino,
“Anthu anu akamapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani ao, kulikonse kumene mungaŵatume, akapemphera kwa Inu Chauta choyang'ana ku mzinda umene Inu mudausankha ndiponso ku Nyumba imene ndakumangiraniyi, yomveketsa dzina lanu,
Anthuwo akabwerera kwa Inu ndi nzeru zao zonse ndi mtima wao wonse, m'dziko la adani ao kumene adaŵatengera ukapolo, ndipo akapemphera kwa Inu choyang'ana ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,
Solomoni adapereka nsembe zachiyanjano kwa Chauta pakupha ng'ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraele onsewo adaipereka Nyumba ya Chauta ija.
Choncho nthaŵi imeneyo Solomoni adachita chikondwerero, pamodzi ndi Aisraele onse. Unali msonkhano waukulu kwambiri, kuyambira ku chipata cha Hamati mpaka ku kamtsinje ka Ejipito. Adachita chikondwerero chimenechi chopembedza Chauta Mulungu wathu, masiku asanu ndi aŵiri.