Mfumu Ahabu anali ndi zidzukulu zazimuna 70 ku Samariya. Tsono Yehu adalemba makalata naŵatumiza ku Samariya kwa olamulira mzindawo, kwa akuluakulu ndiponso kwa anthu amene ankalera zidzukulu za Ahabu kuti,
mwa zidzukulu za mbuyanu musankhule mmodzi wooneka bwino kwambiri ndipo mumloŵetse ufumu wa bambo wake. Kenaka mukonzekere nkhondo kumenyera banja la mbuyanu.”
Tsono Yehu adaŵalemberanso kalata yachiŵiri kuti, “Ngati muli pambuyo panga, ndipo ngati muli okonzeka kundimvera, mudule mitu ya ana a mbuyanu, mudze nayo kwa ine ku Yezireele maŵa nthaŵi yonga yomwe ino.” Ndiye kuti zidzukulu za mfumu 70 zija zinkaleredwa ndi akuluakulu amumzinda aja.
Ndiye akuluakuluwo atalandira kalata ija, adagwira zidzukulu za mfumuzo nkuzipha, 70 zonsezo, naika mitu yao m'madengu, nkuitumiza kwa Yehu ku Yezireele.
Tsono wamthenga adafika nauza Yehu kuti, “Abwera nayo mitu ija ya zidzukulu za mfumuyi.” Apo iyeyo adati, “Kaiwunjikeni m'miyulu iŵiri pa chipata, ndipo ikhale pamenepo mpaka m'maŵa.”
Dziŵani tsono kuti mau a Chauta, amene adanena za banja la Ahabu, sadzapita padera. Ndi Chauta amene wachitadi zimene adalankhula kudzera mwa Eliya mtumiki wake.”
adakumana ndi abale ake a Ahaziya mfumu ya Yuda. Adaŵafunsa kuti, “Nanga inunso ndinu yani?” Iwo adayankha kuti, “Ndife abale a malemu Ahaziya, ndipo tidabwera kudzacheza ndi ana a mfumu Ahabu, ndiponso ana a mfumukazi Yezebele.”
Tsono Yehu adati, “Atengeni amoyo.” Ndipo adaŵatenga amoyo, nakaŵaphera ku chitsime cha ku malo aja a abusaŵa, anthu okwanira 42. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe.
Pambuyo pake Yehu adasonkhanitsa anthu onse a mu mzinda wa Samariya naŵauza kuti, “Ahabu ankatumikira Baala pang'ono chabe. Koma ine Yehu ndidzamtumikira kwambiri.
Koma Yehuyo sadaleke kwenikweni zoipa zimene ankachita mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene ankachimwitsa nazo Aisraele. Sadaleke kupembedza zifanizo zagolide za anaang'ombe zimene zinali ku Betele ndi ku Dani.
Ndipo Chauta adauza Yehu kuti: “Chifukwa choti wachita zondikomera Ine, poononga banja la Ahabu monga momwe ndinkafunira, ana ako adzakhala pa mpando waufumu wa Israele mpaka mbadwo wachinai.”
Koma Yehuyo sankasamala Malamulo a Chauta, Mulungu wa Israele, ndi mtima wake wonse. Adapitirizabe kuchita zoipa zimene Yerobowamu adachimwitsa nazo Aisraele.
Adayambira ku Yordani chakuvuma, nakafika ku Aroere pafupi ndi chigwa cha Arinoni. Dziko limeneli lidaphatikiza madera onse a Giliyadi ndi Basani, kumene zinkakhala zidzukulu za Gadi, Rubeni ndi Manase.