Ndipo Davide anati, Ndidzamcitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wace anandicitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wace. Pofika anyamata ace a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,
akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kucitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? sakudzerani kodi anyamata ace kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?
Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente cikwi cimodzi a siliva, kudzilembera magareta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-maaka, ndi ku Zoba.
Ndipo pakuona anyamata a Hadarezeri kuti Israyeli anawakantha, anapangana mtendere ndi Davide, namtumikira; ndi Aaramu anakana kuthandizanso ana a Amoni.