×

Mawu a Mulungu 2016

1 MBIRI 25

1
Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi:
2
Kuchokera kwa ana a Asafu: Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asareli. Ana a Asafu amalamulidwa ndi Asafu ndipo amanenera moyangʼaniridwa ndi mfumu.
3
Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova.
4
Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake: Bukiya, Mataniya, Uzieli, Subaeli ndi Yerimoti; Hananiya, Hanani, Eliata, Gidaliti ndi Romamiti-Ezeri; Yosibakasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti.
5
Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.
6
Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu.
7
Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288.
8
Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo.
9
Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe, ana ndi abale ake. — 12 Maere achiwiri anagwera Gedaliya, ndi abale ake ndi ana ake. — 12
10
Maere achitatu anagwera Zakuri, ana ake ndi abale ake. — 12
11
Maere achinayi anagwera Iziri, ana ake ndi abale ake. — 12
12
Maere achisanu anagwera Netaniya, ana ake ndi abale ake. — 12
13
Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya, ana ake ndi abale ake. — 12
14
Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela, ana ake ndi abale ake. — 12
15
Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya, ana ake ndi abale ake. — 12
16
Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya, ana ake ndi abale ake. — 12
17
Maere a khumi anagwera Simei, ana ake ndi abale ake. — 12
18
Maere a 11 anagwera Azareli, ana ake ndi abale ake. — 12
19
Maere a 12 anagwera Hasabiya, ana ake ndi abale ake. — 12
20
Maere a 13 anagwera Subaeli, ana ake ndi abale ake. — 12
21
Maere a 14 anagwera Matitiya, ana ake ndi abale ake. — 12
22
Maere a 15 anagwera Yeremoti, ana ake ndi abale ake. — 12
23
Maere a 16 anagwera Hananiya, ana ake ndi abale ake. — 12
24
Maere a 17 anagwera Yosibakasa, ana ake ndi abale ake. — 12
25
Maere a 18 anagwera Hanani, ana ake ndi abale ake. — 12
26
Maere a 19 anagwera Maloti, ana ake ndi abale ake. — 12
27
Maere a 20 anagwera Eliyata, ana ake ndi abale ake. — 12
28
Maere a 21 anagwera Hotiri, ana ake ndi abale ake. — 12
29
Maere a 22 anagwera Gidaliti, ana ake ndi abale ake. — 12
30
Maere a 23 anagwera Mahazioti, ana ake ndi abale ake. — 12
31
Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri, ana ake ndi abale ake — 12.
Chewa Bible 2016
The Word of God in Contemporary Chichewa 2002, 2016 by Biblica, Inc
:
Sungani Zolemba