Ndipo ana a Israyeli monga mwa ciwerengo cao, kunena za akuru a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu nchito iri yonse ya magawidwe, akulowa ndi kuturuka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya caka, cigawo ciri conse nca amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.
Woyang'anira cigawo ca mwezi waciwiri ndiye Dodai M-ahohi ndi cigawo cace; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m'cigawo cace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
Kazembe wacitatu wa khamu wa mwezi wacitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkuru; ndi m'cigawo mwacemunalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai.
Wacinai wa mwezi wacinai ndiye Asebeli mbale wa Yoabu, ndi pambuyo pace Zebadiya mwana wace; ndi m'cigawo mwace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.
Yoabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsiriza; ndi mkwiyo unagwera Israyeli cifukwa ca ici, ndipo ciwerengo cao sicinalembedwa m'buku la mbiri ya mfumu Davide.
Ndipo woyang'anira cuma ca mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyeli, ndi woyang'anira wa cuma ca m'minda, m'mizinda ndi m'miraga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;