Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zocuruka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Gileadi.
Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Yimla. Nati Yehosafati, Isatero mfumu.
Mfumu ya Israyeli tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wacifumu wace, obvala zobvala zacifumu zao, nakhala pamalo poyera polowera pa cipata ca Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.
Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu cokoma ngati m'kamwa m'modzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene cokoma.
Nati iye, Cifukwa cace tamvani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wace wacifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lirikuima pa dzanja lace lamanja, ndi pa dzanja lace lamanzere.
Ndi mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu bvalani zobvala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israyeli, namuka iwo kunkhondo.
Ndipo munthu anaponya mubvi wace ciponyeponye, namlasa pakati pa maluma a maraya ace acitsulo. Potero anati kwa woyendetsa garetayo, Tembenuza dzanja lako, nundicotse ku khamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa.
Ndipo nkhondo inakula tsiku lija; koma mfumu ya Israyeli inagwirizizil ka m'gareta wace popenyana ndi Aaramu mpaka madzulo, namwalira nthawi yakulowa dzuwa.