×

Buku Loyera

2 MBIRI 19

1
Yehosafati mfumu ya ku Yuda adabwerera kunyumba kwake ku Yerusalemu mwamtendere.
2
Koma mneneri Yehu, mwana wa Hanani, adatuluka kuti akumane naye, ndipo adafunsa mfumu Yehosafati kuti, “Kodi ndi bwino kuŵathandiza anthu oipa amene amadana ndi Chauta? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Chauta ulikudza kwa inu.
3
Komabe pali zina zabwino zimene mudachita, pakuti mudaononga mafano a m'dziko muno, ndipo mwakhala mukulimbikira ndi mtima wonse kufunafuna Mulungu.”
4
Yehosafati ankakhala ku Yerusalemu. Adayendera anthu kuchokera ku Beereseba mpaka ku dziko lamapiri la ku Efuremu, naŵabweza kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao.
5
Adaika anthu oweruza m'dzikomo, mu mzinda uliwonse wamalinga wa ku Yuda.
6
Tsono adauza aweruziwo kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, pakuti simukuweruza m'dzina la munthu ai, koma m'dzina la Chauta. Chautayo ali nanu pamene mukuweruza.
7
Tsono khalani anthu oopa Chauta. Muzisamala zimene mukuchita, pakuti Chauta, Mulungu wathu, sapotoza chiweruzo, kapena kukondera, kapenanso kulandira ziphuphu.”
8
Ku Yerusalemuko Yehosafati adaika Alevi ena ndi ansembe ndiponso akulu a mabanja a Aisraele, kuti aziweruza m'dzina la Chauta ndi kugamula milandu ya anthu. Iwoŵa ankakhala ku Yerusalemu.
9
Adaŵalamula kuti, “Muzichita ntchito imeneyi moopa Chauta, mokhulupirika, ndiponso ndi mtima wonse.
10
Pakakhala mlandu wokhudza abale anu amene akukhala m'mizinda yao, monga mlandu wokhetsa magazi, kapena mlandu wa kusamvera malamulo kapena malangizo kapena zogamula zina, muziŵaphunzitsa nthaŵi zonse kuti asamachimwe pamaso pa Chauta. Motero mkwiyo wa Chauta sudzakugwerani inuyo ndi abale anu. Muzichita choncho, ndipo simudzachimwa konse.
11
Tsono Amariya, mkulu wa ansembe, ndiye adzakhale wokutsogolerani pa zonse zokhudza Chauta. Zebadiya mwana wa Ismaele, kazembe wa fuko la Yuda, ndiye aziyang'anira zonse zokhudza mfumu. Ndipo Alevi adzakutumikirani ngati akapitao. Muzichita zimenezi molimba mtima, Chauta akhale naye amene ali wolungama.”
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba