Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo zitatha izi, kunacitika kuti ana a Moabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati. |
| 2 |
| Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukuru wa anthu ocokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni Tamara, ndiwo Engedi. |
| 3 |
| Ndipo Yehosafati anacita mantha, nalunjikitsa nkhope yace kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse. |
| 4 |
| Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anacokera ku midzi yonse ya Yuda kufuna Yehova. |
| 5 |
| Ndipo Yehosafati anaima mu msonkhano wa Ayuda, ndi a ku Yerusalemu, ku nyumba ya Yehova, pakati pa bwalo latsopano; |
| 6 |
| nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m'Mwamba kodi? sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulaka Inu. |
| 7 |
| Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pa maso pa ana anu Israyeli, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha? |
| 8 |
| nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti, |
| 9 |
| Cikatigwera coipa, lupanga, ciweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala ciriri pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kupfuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa. |
| 10 |
| Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Moabu, ndi a ku phiri la Seiri, amene simunalola Israyeli awalowere, pakuturuka iwo m'dziko la Aigupto, koma anawapambukira osawaononga; |
| 11 |
| tapenyani, m'mene atibwezera; kudzatiinga m'colowa canu, cimene munatipatsa cikhale colowa cathu. |
| 12 |
| Mulungu wathu, simudzawaweruza? pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu. |
| 13 |
| Ndipo Ayuda onse anakhala ciriri pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda ao, akazi ao, ndi ana ao. |
| 14 |
| Pamenepo mzimu wa Yehova unagwera Yahazieli mwana wa Zekriya, mwana wa Benaya, mwana wa Yetieli, mwana wa Mataniya, Mlevi, wa ana a Asafu, pakati pa msonkhano; |
| 15 |
| nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala m'Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa cifukwa ca aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. |
| 16 |
| Mawa muwatsikire; taonani, akwera pokwerera pa Zizi, mudzakomana nao polekezera cigwa cakuno ca cipululu ca Yerueli. |
| 17 |
| Si kwanu kucita nkhondo kuno ai; cirimikani, imani, nimupenye cipulumutso ca Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwaturukire, popeza Yehova ali ndi inu. |
| 18 |
| Ndipo Yehosafati anawerama mutu wace, nkhope yace pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala m'Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova. |
| 19 |
| Ndipo Alevi, a ana a Akohati, ndi a ana a Kora, anauka kulemekeza Yehova Mulungu wa Israyeli ndi mau omveketsa. |
| 20 |
| Nalawira mamawa, naturuka kumka ku cipululu ca Tekoa; ndipo poturuka iwo, Yehosafati anakhala ciriri, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala m'Yerusalemu, Hmbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ace, ndipo mudzalemerera. |
| 21 |
| Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oyimbira Yehova, ndi kulemekeza ciyero cokometsetsa, pakuturuka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti cifundo cace cikhala cosatha. |
| 22 |
| Ndipo poyamba iwo kuyimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amoabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha. |
| 23 |
| Pakuti ana a Amoni, ndi a Moabu, anaukira okhala m'phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala m'Seiri, anasandulikirana kuonongana. |
| 24 |
| Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kucipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo iri ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense. |
| 25 |
| Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ace kutenga zofunkha zao, anapezako cuma cambiri, ndi mitembo yambiri, ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinacuruka. |
| 26 |
| Ndi tsiku lacinai anasonkhana m'cigwa ca Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; cifukwa cace anacha dzina lace la malowo, Cigwa ca Beraka, mpaka lero lino. |
| 27 |
| Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kumka ku Yerusalemu ndi cimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao. |
| 28 |
| Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, ku nyumba ya Yehova. |
| 29 |
| Ndipo kuopsa kwa Mulungu kunagwera maufumu onse a m'maiko, pamene anamva kuti Yehova adayambana ndi adani a Israyeli. |
| 30 |
| Nucita bata ufumu wa Yehosafati; pakuti Mulungu wace anampumulitsira pozungulirapo. |
| 31 |
| Momwemo Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda; anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri; ndi dzina la mace ndiye Azuba mwana wa Sili. |
| 32 |
| Ndipo anayenda m'njira ya Asa atate wace osapambukamo, nacita zoongoka pamaso pa Yehova. |
| 33 |
| Komatu misanje siinacotsedwa; popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao. |
| 34 |
| Macitidwe ena tsono adazicita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wochulidwa m'buku la mafumu a Israyeli. |
| 35 |
| Zitathaizi, Yehosafati mfumu ya Yuda anaphatikana ndi Ahaziya mfumu ya Israyeli, yemweyo anacita moipitsitsa; |
| 36 |
| naphatikana naye kupanga zombo zomuka ku Tarisi, nazipanga zombozo m'Ezioni Gebere. |
| 37 |
| Pamenepo Eliezeri mwana wa Dodavahu wa Maresa ananenera kumtsutsa Yehosafati, ndi kuti, Popeza waphatikana ndi Ahaziya Yehova wapasula nchito zako. Ndipo zombo zinasweka zosakhoza kumuka ku Tarisi. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/2chronicles/020.mp3
36
20