Ndipo mfumuyo idati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene wachitadi ndi dzanja lake zimene adaalonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide bambo wanga.
Tsopano Chauta wachitadi zimene adaalonjeza zija. Pakuti ine ndi amene ndaloŵa ufumu m'malo mwa Davide bambo wanga, ndipo ndikulamulira Aisraele pa mpando wa bambo wanga, monga momwe Chauta adaalonjezera. Ndipo ndinedi amene ndamanga Nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele.
Tsono adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, palibe Mulungu wina wonga inu kumwamba kapena pa dziko lapansi. Mumasunga chipangano ndi kuwonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wao wonse.
Tsono Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, mukumbukire zimene zija mudalonjeza bambo wanga, pamene mudati, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israele; malinga ana ako akamasamala mkhalidwe wao ndi kumayenda motsata malamulo anga monga momwe iweyo wayendera pamaso panga.’
Usana ndi usiku maso anu azikhala otsekuka, kuyang'ana Nyumba imeneyi, malo amene Inu mudanena kuti mudzamveketsamo dzina lanu. Imvani pemphero limene mtumiki wanu akupemphera ku malo ano.
Muzimva mapemphero opemba a mtumiki wanu ndiponso a anthu anu Aisraele, akamapemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mutikhululukire.
“Anthu anu Aisraele atagonjetsedwa ndi adani ao chifukwa chakuti adakuchimwirani, pambuyo pake nkutembenuka ndi kutamanda dzina lanu, napemphera ndi kupemba kwa Inu okhala m'Nyumba muno,
Tsono, chodandaula kapena chopembera chingakhale chotani, pempherolo lingakhale la munthu m'modzi kapena la anthu anu onse Aisraele wina aliyense akapemphera mopemba, akuzindikira zovuta za mumtima mwake, natambalitsa manja choloza ku Nyumba ino,
“Anthu anu akamapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani ao, kulikonse kumene mungaŵatume, akapemphera kwa Inu choyang'ana ku mzinda uno umene Inu mudausankha, ndiponso ku Nyumba imene ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,
anthuwo akabwerera kwa Inu ndi maganizo ao onse ndi mtima wao wonse, m'dziko laukapolo kumene iwo aja adaŵatengera, ndipo akapemphera choloza ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha, ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,
“Inu Chauta, dzambatukani tsopano, mupite ku malo anu kumene mumapumulako, Inuyo ndi bokosi la mphamvu zanu. Inu Chauta, ansembe anu avale chilungamo, anthu okutumikirani akondwe nazo zabwino zanu.