Ndipo Aisraele onse ataona moto wotsika kumwambawo, pamodzi ndi ulemerero wa Chauta m'Nyumba ya Chauta ija, adaŵerama, nazyolikitsa nkhope zao pansi, ndipo adapembedza nathokoza Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.”
Tsono Solomoni adapatula malo apakatikati a bwalo lija lokhala kumaso kwa Nyumba ya Chauta, ndipo kumeneko adaperekako nsembe zopsereza ndiponso mafuta a nsembe zachiyanjano, chifukwa chakuti pa guwa lamkuŵa limene adapanga Solomoni lija, panalibe malo oti nkukhalapo nsembe zonse zopsereza ndi zopereka za chakudya, pamodzi ndi mafuta omwe.
Nthaŵi imeneyo Solomoni adachita chikondwerero cha masiku asanu ndi aŵiri pamodzi ndi Aisraele onse. Unali msonkhano waukulu kwambiri, kuyambira ku chipata cha ku Hamati mpaka ku kamtsinje wa ku Ejipito.
Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiŵiriwo, Solomoni adauza anthu aja kuti apite kwao. Anthuwo anali okondwa ndiponso a mtima wosangalala, chifukwa cha zokoma zimene Chauta adaachitira Davide ndi Solomoni ndiponso Aisraele, anthu ake.
Motero Solomoni adamaliza kumanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu ndipo zonse zimene adaaganiza kuti achite m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba yake adazimalizadi mokhoza kwambiri.
ukatero Ine ndidzaukhazikitsa mpando wako waufumu, monga momwe ndidalonjezera Davide bambo wako kuti, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wolamulira Israele.’