Zitapita zaka zambiri, pamene Arita-kisereksesi anali mfumu ya ku Persiya, panali wansembe wina dzina lake Ezara. Iyeyu anali mdzukulu wa Aaroni, mkulu wa ansembe woyamba wa Israele. Makolo ake anali aŵa: Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
Tsono chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Arita-kisereksesi, Ezarayo adanyamuka kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Aisraele ena, ndiye kuti ansembe ndi Alevi, oimba nyimbo, alonda ndiponso anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu.
Pakuti ine mfumu pamodzi ndi aphungu anga asanu ndi aŵiri tikukutuma kuti ukafunsitse za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu, kuti ukaone m'mene anthu akutsatira malamulo amene Mulungu wako adaŵapereka kwa iwe.
Utengenso siliva ndi golide yense amene mumpeze m'dziko lonse la Babiloni, ndiponso zopereka zimene anthu ndi ansembe adzapereka mwaufulu, mosakakamiza, kuperekera Nyumba ya Mulungu wao ya ku Yerusalemu.
Tsono ndi ndalama zimenezi, mudzagule mwachangu ng'ombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zake zaufa ndiponso nsembe zake zazakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa la ku Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu.
Ndipo china chilichonse chimene chingafunikire m'Nyumba ya Mulungu wanu, chimene mudzapeze danga loperekera, ndalama zake zogulira zidzatuluke m'thumba la chuma cha mfumu.
“Tsono ine, mfumu Arita-kisereksesi, ndikulamula onse osunga chuma m'dera la Patsidya pa Yufurate, kuti zonse zimene wansembe Ezara, wophunzira wa malamulo a Mulungu Wakumwamba, adzapemphe kwa inu, zichitike mwachangu.
Zonse zimene Mulungu Wakumwamba alamule, zichitike mwachangu ku Nyumba ya Mulungu Wakumwamba, kuwopa kuti mkwiyo wake ungayakire mfumu ndi dziko lake ndi ana ake.
Ezara adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa makolo athu, amene adaika nzeru zotere mu mtima wa mfumu, kuti apereke ulemu ku Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu.