Zitachitika zimenezi, atsogoleri ena adadza kwa ine, nati, “Aisraele, ansembe ndi Alevi sadadzipatule kwa anthu a mitundu iyi yoyandikana nafe: Akanani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aejipito ndi Aamori. Anthu athuwo akuchita nawo zonyansa zaozo.
Aisraele ena ndi ana ao aamuna adayamba kukwatira ana aakazi a anthuwo. Motero mtundu wathu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a m'maikowo. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo amene akupambana pa kusakhulupirika kumeneku.”
Ndidakhala pansi choncho kufikira nthaŵi yamadzulo. Tsono anthu onse amene ankaopa mau a Mulungu wa Israele, ataona kusakhulupirika kwa obwerako ku ukapolo aja, adayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.
Koma tsopano pa kanthaŵi kochepaka, Inu Chauta, Mulungu wathu, mwaonetsa kukoma mtima kwanu. Mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kuloŵa m'malo anu oyera. Mwatilimbitsa mtima ndi kutitsitsimutsa kwa kanthaŵi mu ukapolo wathu.
Inde ndife akapolo, komabe Inu Mulungu wathu simudatisiya mu ukapolo, mwatiwonetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Persiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu, Inu Mulungu wathu, pa mabwinja ake akale. Mwatitchinjiriza m'dziko la Yudeya ndiponso mu Yerusalemu.
amene mudatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki anu. Mudaŵauza kuti, ‘Dziko mukuloŵamo kuti mulilandelo ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya anthu a m'maikomo. Adzaza dziko lonselo ndi zoipa zaozo.
Nchifukwa chake musakwatitse ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, ndipo ana ao aakazi asakwatiwe ndi ana anu aamuna. Musakhale nawo mumtendere kapena kugwirizana nawo pa malonda, ngati mufuna kukhala amphamvu ndi kumadya zabwino za m'dzikomo, ndi kusiyira ana anu dziko limeneli kuti likhale choloŵa chao mpaka muyaya.’
Inde zonsezi zatigwera kaamba ka ntchito zathu zoipa ndi uchimo wathu waukulu. Komabe Inu Mulungu wathu, mwangotilanga pang'ono, kuyerekeza ndi kukula kwa kuchimwa kwathu, ndipo mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke.