|
| 1 |
|
| Mtima wanga ulema nao moyo wanga, Ndidzadzilolera kudandaula kwanga, Ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga. |
|
| 2 |
|
| Ndidzati kwa Mulungu, Musanditsutse; Mundidziwitse cifukwa ca kutsutsana nane. |
|
| 3 |
|
| Cikukomerani kodi kungosautsa, Kuti mupeputsa nchito yolemetsa manja anu, Ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa? |
|
| 4 |
|
| Muli nao maso a thupi kodi? Mupenya kodi monga umo apenyera munthu? |
|
| 5 |
|
| Masiku anu akunga masiku a munthu kodi, Zaka zanu zikunga masiku a munthu; |
|
| 6 |
|
| Kuti mufunsa mphulupulu yanga, Ndi kulondola coipa canga; |
|
| 7 |
|
| Cinkana mudziwa kuti sindiri woipa, Ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu? |
|
| 8 |
|
| Manja anu anandiumba, nandiulunga monsemu, Koma mufuna kundiononga. |
|
| 9 |
|
| Mukumbukile kuti mwandiumba ngati dothi; Ndipo kodi mudzandibwezera kupfumbi? |
|
| 10 |
|
| Simunanditsanula kodi ngati mkaka, Ndi kundilimbitsa ngati mase? |
|
| 11 |
|
| Munandibveka khungu ndi mnofu, Ndi kundilumikiza mafupa ndi mitsempha, |
|
| 12 |
|
| Mwandipatsa moyo, ndi kundikomera mtima, Ndi masamalidwe anu anasunga mzimu wanga. |
|
| 13 |
|
| Koma izi munazibisa mumtima mwamu; Ndidziwa kuti ici muli naco: |
|
| 14 |
|
| Ndikacimwa mundipenya; Ndipo simudzandimasula mphulupulu yanga. |
|
| 15 |
|
| Ndikakhala woipa, tsoka ine; Ndikakhala wolungama, sindidzakweza mutuwanga; Ndadzazidwa ndi manyazi, Koma penyani kuzunzika kwanga. |
|
| 16 |
|
| Ndipo mutu wanga ukadzikweza, mundisaka ngati mkango; Mubweranso ndi kudzionetsera modabwiza kwa ine. |
|
| 17 |
|
| Mundikonzeranso mboni zonditsutsa, Ndi kundicurukitsira mkwiyo wanu; Nkhondo yobwereza-bwereza yandigwera. |
|
| 18 |
|
| Potero munandibadwitsa cifukwa ninji? Mwenzi nditapereka moyo wanga, lisanandione diso. |
|
| 19 |
|
| Ndikadakhala monga ngati sindikadakhala; Akadanditenga pobadwapo kumka nane kumanda. |
|
| 20 |
|
| Masiku anga satsala owerengeka nanga? lindani, Bandilekani kuti nditsitsimuke pang'ono, |
|
| 21 |
|
| Ndisanacoke kumka kumene sindikabweranso, Ku dziko la mdima ndi la mthunzi wa imfa; |
|
| 22 |
|
| Dziko la mdima bii ngati mdima wandiweyani, Dziko la mthunzi wa imfa losalongosoka, Kumene kuunika kukunga mdima. |
|
|
|
|