|
| 1 |
|
| Pamenepo Yobu anayankha, nati, |
|
| 2 |
|
| Zoonadi inu ndinu anthu, Ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu. |
|
| 3 |
|
| Koma inenso ndiri nayo nzeru monga inu. Sindingakucepereni; Ndani sadziwa zonga izi? |
|
| 4 |
|
| Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wace, Ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha; Munthu wolungama wangwiro asekedwa. |
|
| 5 |
|
| Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwace, Limlindira woterereka mapazi ace. |
|
| 6 |
|
| Mahema a acifwamba akhala mumtendere, Ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima: Amene Mulungu amadzazira dzanja lao. |
|
| 7 |
|
| Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza, Ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza; |
|
| 8 |
|
| Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza; Ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera, |
|
| 9 |
|
| Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse; Kuti dzanja la Yehova licita ici? |
|
| 10 |
|
| M'dzanja mwace muli mpweya wa zamoyo zonse, Ndi mzimu wa munthu ali yense. |
|
| 11 |
|
| M'khutumu simuyesa mau, Monga m'kamwa mulawa cakudya cace? |
|
| 12 |
|
| Kwa okalamba kuli nzeru, Ndi kwa a masiku ocuruka luntha. |
|
| 13 |
|
| Kwa Iye kuli nzeru ndi mphamvu; Uphungu ndi luntha ali nazo. |
|
| 14 |
|
| Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso; Amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira, |
|
| 15 |
|
| Taona atsekera madzi, naphwa; Awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi. |
|
| 16 |
|
| Kwa Iye kuli mphamvu ndi nzeru. Wonyengedwa ndi wonyenga yemwe ali ace. |
|
| 17 |
|
| Apita nao maphungu atawafunkhira, Napulukiritsa oweruza milandu. |
|
| 18 |
|
| Amasula comangira ca mafumu, Nawamangira nsinga m'cuuno mwao. |
|
| 19 |
|
| Apita nao, ansembe atawafunkhica, Nagubuduza amphamvu. |
|
| 20 |
|
| Amcotsera wokhulupirika kunena kwace. Nalanda luntha la akulu. |
|
| 21 |
|
| Atsanulira mnyozo pa akalonga, Nawasezera olimba lamba lao. |
|
| 22 |
|
| Abvumbulutsa zozama mumdima, Naturutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera; |
|
| 23 |
|
| Acurukitsa amitundu, nawaononganso; Abalalikitsa amitundu, nawabwezanso. |
|
| 24 |
|
| Awacotsera akulu a anthu a padziko mtima wao, Nawasokeretsa m'cipululu copanda njira. |
|
| 25 |
|
| Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika, Ndipo awayendetsa dzandi dzandi. |
|
|
|
|