|
| 1 |
|
| Munthu wobadwa ndi mkazi Ngwa masiku owerengeka, nakhuta mabvuto, |
|
| 2 |
|
| Aturuka ngati duwa, nafota; Athawa ngati mthunzi, osakhalitsa. |
|
| 3 |
|
| Ndipo kodi mumtsegulira maso anu wotereyo, Ndi kunditenga kunena nane mlandu Inu? |
|
| 4 |
|
| Adzaturutsa coyera m'cinthu codetsa ndani? nnena mmodzi yense. |
|
| 5 |
|
| Popeza masiku ace alembedwa, ciwerengo ca miyezi yace cikhala ndi Inu, Ndipo mwamlembera malire ace, kuti asapitirirepo iye; |
|
| 6 |
|
| Mumleke osamthira maso, kuti apumule, Kuti akondwere nalo tsiku lace monga wolembedwa nchito. |
|
| 7 |
|
| Pakuti akaulikha mtengo pali ciyembekezo kuti udzaphukanso, Ndi kuti nthambi yace yanthete siidzasowa. |
|
| 8 |
|
| Ngakhale muzu wace wakalamba m'nthaka, Ndi tsinde lace likufa pansi; |
|
| 9 |
|
| Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka, Nudzaswa nthambi ngati womera. |
|
| 10 |
|
| Koma munthu akufa atacita liondeonde Inde, munthu apereka mzimu wace, ndipo ali kuti? |
|
| 11 |
|
| Madzi acoka m'nyanja, Ndi mtsinje ukuphwa, nuuma; |
|
| 12 |
|
| Momwemo munthu agona pansi, osaukanso; Kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso, Kapena kuutsidwa pa tulo tace. |
|
| 13 |
|
| Ha! mukadandibisa kumanda, Mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira. |
|
| 14 |
|
| Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, Mpaka kwafika kusandulika kwanga, |
|
| 15 |
|
| Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; Mukadakhumba nchito ya manja anu. |
|
| 16 |
|
| Koma tsopano muwerenga maponda mwanga; Kodi simuyang'anitsa cimo langa? |
|
| 17 |
|
| Colakwa canga caikidwa m'thumba lokomedwa cizindikilo; Ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga. |
|
| 18 |
|
| Ndipo zoonadi, likagwa phiri, latha; Ndi thanthwe lisunthika m'malo mwace; |
|
| 19 |
|
| Madzi anyenya miyala; Zosefukira zao zikokolola pfumbi la nthaka; Ndipo muononga ciyembekezo ca munthu. |
|
| 20 |
|
| Mumlaka cilakire, napita iye; Musintha nkhope yace, mumuuza acoke. |
|
| 21 |
|
| Ana ace aona ulemu osadziwa iye; Napeputsidwa, koma osazindikira za iwo. |
|
| 22 |
|
| Koma thupi lace limuwawira yekha, Ndi mtima wace umliritsa yekha. |
|
|
|
|