|
| 1 |
|
| Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati, |
|
| 2 |
|
| Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika, Ndi kudzaza mimba yace ndi mphepo ya kum'mawa? |
|
| 3 |
|
| Kodi atsutsane ndi mnzace ndi mau akusathandiza? Kapena ndi maneno akusaphindulitsa? |
|
| 4 |
|
| Zedi uyesa cabe mantha, Nucepsa cilingiriro pamaso pa Mulungu. |
|
| 5 |
|
| Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako, Nusankha lilime la ocenjerera. |
|
| 6 |
|
| Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai. Inde milomo yako ikucitira umboni wakukutsutsa. |
|
| 7 |
|
| Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa? Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri? |
|
| 8 |
|
| Kodi unamva uphungu wacinsinsi wa Mulungu? Ndipo unadzikokera nzeru kodi? |
|
| 9 |
|
| Udziwa ciani, osacidziwa ife? Uzindikira ciani, cosakhala mwa ife? |
|
| 10 |
|
| Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa, Akuposa atate wako masiku ao, |
|
| 11 |
|
| Masangalatso a Mulungu akucepera kodi? Kapena uli naco cinsinsi kodi? |
|
| 12 |
|
| Mtima wako usonthokeranji nawe? Maso ako aphethira-phethira cifukwa ninji? |
|
| 13 |
|
| Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu, Ndi kulola mau otere aturuke m'kamwa mwako. |
|
| 14 |
|
| Munthu nciani kuti akhale woyera, Wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama? |
|
| 15 |
|
| Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ace; Ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pace, |
|
| 16 |
|
| Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, Wakumwa cosalungama ngati madzi. |
|
| 17 |
|
| Ndidzakuonetsa, undimvere; Cimene ndinaciona, ndidzakufotokozera; |
|
| 18 |
|
| Cimene adacinena anzeru, Adacilandira kwa makolo ao, osacibisa; |
|
| 19 |
|
| Ndiwo amene analandira okha dzikoli, Wosapita mlendo pakati pao; |
|
| 20 |
|
| Munthu woipa adzipweteka masiku ace onse, Ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa. |
|
| 21 |
|
| M'makutu mwace mumveka zoopsetsa; Pali mtendere amfikira wakumuononga. |
|
| 22 |
|
| Sakhulupirira kuti adzaturukamo mumdima, Koma kuti lupanga limlindira; |
|
| 23 |
|
| Ayendayenda ndi kufuna cakudya, nati, Ciri kuti? Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima, |
|
| 24 |
|
| Nsautso ndi cipsinjo zimcititsa mantha, Zimlaka ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo; |
|
| 25 |
|
| Pakuti amtambasula dzanja lace moyambana ndi Mulungu, Napikisana ndi Wamphamvuyonse. |
|
| 26 |
|
| Amthamangira Iye mwaliuma, Ndi zikopa zace zocindikira. |
|
| 27 |
|
| Popeza anakuta nkhope yace ndi kunenepa kwace, Nacita mafunyenye a mafuta m'zuuno zace; |
|
| 28 |
|
| Adzakhala m'midzi yopasuka, M'nyumba zosakhalamo munthu, Zoti zisandulika muunda. |
|
| 29 |
|
| Sadzakhala wolemera, ndi cuma cace sicidzakhalitsa, Ndi zipatso zace sizidzacuruka padziko. |
|
| 30 |
|
| Sadzacoka mumdima; Lawi la moto lidzaumitsa nthambi zace; Ndipo adzacoka ndi mpumo wa m'kamwa mwace. |
|
| 31 |
|
| Asatame zopanda pace, kudzinyenga nazo; Pakuti zopanda pace zidzakhala combwezera cace. |
|
| 32 |
|
| Cidzacitika isanadze nthawi yace; Pakuti nthambi yace siidzaphuka. |
|
| 33 |
|
| Adzayoyoka zipatso zace zosapsa ngati mpesa, Nadzathothoka maluwa ace ngati mtengo wazitona. |
|
| 34 |
|
| Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala cumba, Ndi moto udzapsereza mahema a olandira cokometsera mlandu. |
|
| 35 |
|
| Aima ndi cobvuta, nabala mphulupulu, Ndi m'mimba mwao mukonzeratu cinyengo. |
|
|
|
|