|
| 1 |
|
| Pamenepo Yobu anayankha, nati, |
|
| 2 |
|
| Ndamva zambiri zotere; Inu nonse ndinu otonthoza mtima mondilemetsa. |
|
| 3 |
|
| Kodi adzatha mau ouluzika? Kapena cikuwindula nciani kuti uyankha zotere? |
|
| 4 |
|
| Inenso ndikadanena monga inu, Moyo wanu ukadakhala m'malo mwa moyo wanga, Ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu, Ndi kukupukusirani mutu wanga. |
|
| 5 |
|
| Koma ndikadakulimbikitsani ndi m'kamwa mwanga, Ndi citonthozo ca milomo yanga cikadatsitsa cisoni canu. |
|
| 6 |
|
| Cinkana ndinena cisoni canga sicitsika; Ndipo ndikaleka, cindicokera nciani? |
|
| 7 |
|
| Koma tsopano wandilemetsa Iye; Mwapasula msonkhano wanga wonse. |
|
| 8 |
|
| Kundigwira kwanu, ndiko umboni wonditsutsa, Kuonda kwanga kundiukira, kucita umboni pamaso panga. |
|
| 9 |
|
| Iye ananding'amba m'kundida kwace, nakwiya nane, Anandikukutira mano; Mdani wanga ananditong'olera maso ace. |
|
| 10 |
|
| Iwo anandiyasamira pakamwa pao; Anandiomba pama ndi kunditonza; Asonkhana pamodzi kunditsutsa. |
|
| 11 |
|
| Mulungu andipereka kwa osalungama, Nandiponya m'manja a oipa. |
|
| 12 |
|
| Ndinali mkupuma, koma anandityola; Inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya; Anandiimika ndikhale candamali. |
|
| 13 |
|
| Eni mauta ace andizinga, Ang'amba imso zanga, osazileka; Natsanulira pansi ndulu yanga. |
|
| 14 |
|
| Andipasula-pasula; Andithamangira ngati wamphamvu. |
|
| 15 |
|
| Ndadzisokerera ciguduli ku khungu langa, Ndipo ndaipsa mphamvu yanga m'pfumbi. |
|
| 16 |
|
| Nkhope yanga njodetsedwa ndi kulira misozi, Ndi pa zikope zanga pali mthunzi wa imfa; |
|
| 17 |
|
| Pangakhale palibe ciwawa m'manja mwanga, Ndi pemphero langa ndi loyera. |
|
| 18 |
|
| Dziko iwe, usakwirire mwazi wanga, Ndi kulira kwanga kusowe popumira. |
|
| 19 |
|
| Tsopanonso, taona, mboni yanga iri kumwamba, Ndi nkhoswe yanga ikhala m'mwamba. |
|
| 20 |
|
| Mabwenzi anga andinyoza; Koma diso langa lilirira misozi kwa Mulungu; |
|
| 21 |
|
| Ha! munthu akadapembedzera mnzace kwa Mulungu, Monga munthu apembedzera mnansi wace! |
|
| 22 |
|
| Pakuti zitafika zaka zowerengeka, Ndidzamuka ku njira imene sindibwererako. |
|
|
|
|