Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Mzimu wanga watha, masiku anga afafanizika, Kumanda kwandikonzekeratu. |
| 2 |
| Zoonadi, ali nane ondiseka; Ndi diso langa liri cipenyere m'kundiwindula kwao. |
| 3 |
| Mupatse cigwiriro tsono, mundikhalire cikole Inu nokha kwanu; Ndani adzapangana nane kundilipirira? |
| 4 |
| Pakuti mwabisira mtima wao nzeru; Cifukwa cace simudzawakuza. |
| 5 |
| Iye wakupereka mabwenzi ace kuukapolo, M'maso mwa ana ace mudzada. |
| 6 |
| Anandiyesanso nthanthi za anthu; Ndipo ndakhala ngati munthu womthira malobvu pankhope pace. |
| 7 |
| M'diso mwanga mucita cizirezire cifukwa ca cisoni, Ndi ziwalo zanga zonse ziribe cithunzi. |
| 8 |
| Anthu oongoka mtima adzadabwa naco, Ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsotsa wonyoza Mulunguyo. |
| 9 |
| Koma wolungama asungitsa njira yace, Ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu. |
| 10 |
| Koma bwerani inu nonse, idzani tsono; Pakuti sindipeza mwa inu wanzeru. |
| 11 |
| Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka, Zace zace zomwe za mtima wanga. |
| 12 |
| Zisanduliza usiku ukhale usana; Kuunika kuyandikana ndi mdima. |
| 13 |
| Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga; Ndikayala pogona panga mumdima. |
| 14 |
| Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga; Kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga; |
| 15 |
| Ciri kuti ciyembekezo canga? Inde, ciyembekezo canga adzaciona ndani? |
| 16 |
| Cidzatsikira ku mipingiridzo ya kumanda, Pamene tipumulira pamodzi kupfumbi. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/job/017.mp3
42
17