|
| 1 |
|
| Tsono Bilidadi wa ku Suki adayankha kuti, |
|
| 2 |
|
| “Kodi iwe Yobe, ukhala mpaka liti ukufunafuna zonena? Ingokhala chete, umvetsere, ndipo ife tilankhula. |
|
| 3 |
|
| Chifukwa chiyani ukutiyesa opusa ngati ng'ombe? Chifukwa chiyani tikuwoneka ngati opanda nzeru m'maso mwako? |
|
| 4 |
|
| Iwe ukungodzipweteka ndi mkwiyo wako. Kodi dziko lapansi lidzasanduka bwinja chifukwa choti iweyo uli wokwiya? Kodi thanthwe nkudzachotsedwa pamalo pake, kuti likukondweretse iweyo? |
|
| 5 |
|
| “Nyale ya munthu woipa yazima, malaŵi a moto wake sakuŵalanso. |
|
| 6 |
|
| Kuŵala kwa m'nyumba mwake kwasanduka mdima, ndipo nyale ya pambali pake yazima. |
|
| 7 |
|
| Kale ankayenda ndi mgugu, koma tsopano wakhumudwa. Nzeru zake zomwe zamgwetsa. |
|
| 8 |
|
| Mapazi ake omwe amloŵetsa mu ukonde, ndipo wakodwa. Tsono kuti achokemo, wagweranso m'mbuna. |
|
| 9 |
|
| Msampha wamkola mwendo, ndipo khwekhwe lamgwira. |
|
| 10 |
|
| Amtchera msampha pansi mobisika, amtchera diŵa m'njira. |
|
| 11 |
|
| Zoopsa zikumchititsa mantha pa mbali zonse, zikumtsatira pambuyo pake. |
|
| 12 |
|
| Adaali ndi mphamvu, koma tsopano ali ndi njala. Tsoka likumdikira nthaŵi zonse. |
|
| 13 |
|
| Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse, miyendo yake, manja ake, zonse zaola. |
|
| 14 |
|
| Amuchotsa m'nyumba mwake m'mene ankadalira. Amkokera kwa Imfa, mfumu ya zoopsa zonse. |
|
| 15 |
|
| M'nyumba mwake zake zonse zachotsedwamo, awazamo sulufule, kuti aphe tizilombo ta matenda. |
|
| 16 |
|
| Mizu yake ikuuma pansi, nthambi zake zikufota. |
|
| 17 |
|
| Sadzamkumbukiranso kwao kapena kwina kulikonse, dzina lake lidzaiŵalika. |
|
| 18 |
|
| Adzamchotsa m'dziko la amoyo ndi kumponya mu mdima, adzampirikitsa pa dziko lapansi. |
|
| 19 |
|
| Sadzaona zidzukulu m'banja mwake. Sikudzaoneka ana otsala kumene ankakhalako. |
|
| 20 |
|
| Anthu akuzambwe adabwa nalo tsoka lakelo, anthu akuvuma nawonso akungopukusa mitu. |
|
| 21 |
|
| Ndithu zimenezi ndizo zimagwera anthu oipa. Kumeneku ndiye kutha kwake kwa anthu osasamala za Mulungu.” Yobe |
|
|
|
|