Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Koma Yobu anayankha, nati, |
| 2 |
| Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa; Kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m'kulemera kwace. |
| 3 |
| Ha! ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu, Kuti ndifike ku mpando wace! |
| 4 |
| Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pace, Ndikadadzaza m'kamwa mwanga ndi matsutsano. |
| 5 |
| Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine, Ndikadazindikira cimene akadanena nane. |
| 6 |
| Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yace yaikuru? Iai, koma akadandicherera khutu. |
| 7 |
| Apo woongoka mtima akadatsutsana naye; Ndipo ndikadapulumuka cipulumukire kwa Woweruza wanga. |
| 8 |
| Taonani, ndikamka m'tsogolo, kulibe Iye; Kapena m'mbuyo sindimzindikira; |
| 9 |
| Akacita Iye kulamanzere, sindimpenyerera; Akabisala kulamanja, sindimuona, |
| 10 |
| Koma adziwa njira ndilowayi; Atandiyesa ndidzaturuka ngati golidi. |
| 11 |
| Phazi langa lagwiratu moponda Iye, Ndasunga njira yace, wosapambukamo. |
| 12 |
| Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yace; Ndasungitsa mau a pakamwa pace koposa lamulo langa langa. |
| 13 |
| Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani? Ndi ici cimene moyo wace ucifuna acicita. |
| 14 |
| Pakuti adzacita condiikidwiratu; Ndipo zambiri zotere ziri ndi Iye. |
| 15 |
| Cifukwa cace ndiopsedwa pankhope pace; Ndikalingirira, ndicita mantha ndi Iye. |
| 16 |
| Pakuti Mulungu walefula mtima wanga, Ndi Wamphamvuyonse wandiopsa. |
| 17 |
| Popeza sindinalikhidwa usanafike mdimawo, Ndipo sanandiphimbira nkhope yanga ndi mdima wa bii. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/job/023.mp3
42
23