Buku Loyera
|
| 1 |
| Apo Yobe adayankha kuti, |
| 2 |
| “Leronso ndikudandaula kwambiri kwa Mulungu. Ngakhale ndikubuula, Mulungu akundilangiralangira ndithu. |
| 3 |
| Ha, ndikadadziŵa kumene ndikadampeza Mulungu, kuti ndikafike mpaka komwe amakhalako! |
| 4 |
| Ndikadakamba mlandu wanga pamaso pake, bwenzi nditafotokoza zifukwa zanga zonse. |
| 5 |
| Bwenzi nditamva mau amene akadandiyankha, bwenzi nditamvetsa zimene akadandiwuza. |
| 6 |
| Kodi Mulungu akadalimbana nane ndi mphamvu zake? Ai, koma akadamva mau anga. |
| 7 |
| Kumeneko munthu wolungama akadalankhula ndi Iye modekha. Wondiweruzayo akadandipeza wosalakwa nthaŵi zonse. |
| 8 |
| “Taonani, ndikapita chakutsogolo, Iye kulibe kumeneko, ndikabwerera cham'mbuyo, sinditha kumupenya. |
| 9 |
| Ndimamfunafuna kumanzere, koma osamuwona. Ndimayang'ananso kumanja, koma osampenya ndithu. |
| 10 |
| Komabe Mulungu amadziŵa m'mene ndimayendera, akandiyesa adzapeza kuti ndine wangwiro ngati golide. |
| 11 |
| Mapazi anga akuponda m'mapazi mwake, ndasunga njira yake, ndipo sindidaitaye. |
| 12 |
| Sindidapatuke kusiya malamulo ake. Ndasunga mau a pakamwa pake kupambana zofuna zanga zonse. |
| 13 |
| “Iyeyo ndi wosasinthika, nanga ndani angathe kumsintha maganizo? Zimene wafuna, amazichitadi. |
| 14 |
| Zimene adatsimikiza kuti adzandichita, adzachitadi, ndipo amalingalira zambiri zoterezi. |
| 15 |
| Nchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake. Ndikaganiza za iyeyo, ndimaopa kwabasi. |
| 16 |
| Mulungu walefula mtima wanga. Mphambe wandiwopsa. |
| 17 |
| Wandichititsa mantha ndi Mulungu, osati mdima wa mavuto onse amene amandiphimbaŵa.” |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/job/023.mp3
42
23