|
| 1 |
|
| Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo? Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ace? |
|
| 2 |
|
| Alipo akusendeza malire; Alanda gulu la zoweta, nazidyetsa. |
|
| 3 |
|
| Akankhizira kwao buru wa amasiye, Atenga ng'ombe ya mfedwa ikhale cikole. |
|
| 4 |
|
| Apambukitsa aumphawi m'njira; Osauka a padziko abisala pamodzi. |
|
| 5 |
|
| Taonani, ngati mbidzi za m'cipululu Aturukira ku nchito zao, nalawirira nkufuna cakudya; Cipululu ciwaonetsera cakudya ca ana ao. |
|
| 6 |
|
| Atema dzinthu zao m'munda; Natola khunkha m'munda wampesa wa woipa. |
|
| 7 |
|
| Agona amarisece usiku wonse opanda cobvala, Alibe copfunda pacisanu. |
|
| 8 |
|
| Abvumbwa ndi mvula kumapiri, Nafukata thanthwe posowa pousapo. |
|
| 9 |
|
| Akwatula wamasiye kubere, Natenga cikole cobvala ca osauka; |
|
| 10 |
|
| Momwemo ayenda amarisece opanda cobvala, Nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala. |
|
| 11 |
|
| M'kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta; Aponda mphesa moponderamo, namva ludzu. |
|
| 12 |
|
| M'mudzi waukuru anthu abuula alinkufa; Ndi moyo wa iwo olasidwa upfuula; Koma Mulungu sasamalira coipaco. |
|
| 13 |
|
| Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika, Sadziwa njira zace, Sasunga mayendedwe ace. |
|
| 14 |
|
| Kukaca auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi; Ndi usiku asanduka mbala. |
|
| 15 |
|
| Ndipo diso la wacigololo liyombekezera cisisira, Ndi kuti, Palibe diso lidzandiona; Nabvala cophimba pankhope pace. |
|
| 16 |
|
| Kuli mdima aboola nyumba, Usana adzitsekera, Osadziwa kuunika. |
|
| 17 |
|
| Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa; Pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa. |
|
| 18 |
|
| Atengedwa ngati coyandama pamadzi; Gawo lao litembereredwa padziko; Sadzalunjikanso njira ya minda yamphesa. |
|
| 19 |
|
| Cirala ndi dzuwa zitha madzi a cipale cofewa, Momwemo manda acita nao ocimwa. |
|
| 20 |
|
| M'mimba mudzamuiwala; mphutsi zidzamudya mokondwera. Sadzamkumbukilanso; Ndipo cosalungama cidzatyoledwa ngati mtengo. |
|
| 21 |
|
| Alusira cumba wosabala, Osamcitira wamasiye cokoma. |
|
| 22 |
|
| Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yace; Iwo aukanso m'mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo. |
|
| 23 |
|
| Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo; Koma maso ace ali pa njira zao. |
|
| 24 |
|
| Akwezeka; m'kamphindi kuti zi; Inde atsitsidwa, acotsedwa monga onse ena, Adutidwa ngati tirigu ngala zace. |
|
| 25 |
|
| Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndiri wabodza, Ndi kuyesa mau anga opanda pace? |
|
|
|
|