×

Buku Lopatulika 1992

YOBU 25

1
Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,
2
Kulamulira ndi kuopsa kuti ndi Iye; Acita mtendere pa zam'mwamba zace.
3
Ngati awerengedwa makamu ace? Ndipo ndaniyo, kuunika kwace sikumturukira?
4
Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?
5
Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala; Ndi nyenyezi siziyera pamaso pace;
6
Kopambana kotani nanga munthu, ndiye mphutsi! Ndi wobadwa ndi munthu, ndiyo nyongolotsi!
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba