Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Koma Yobu anayankha, nati, |
| 2 |
| Wamthandiza bwanji wopanda mphamvu, Kulipulumutsa dzanja losalimba! |
| 3 |
| Wampangira bwanji wopanda nzeruyu! Ndi kudziwitsa nzeru zeni zeni mocurukal |
| 4 |
| Wafotokozera yani mau? Ndi mzimu wa yani unaturuka mwa iwe? |
| 5 |
| Adafawo anjenjemera Pansi pa madzi ndi zokhalamo, |
| 6 |
| Kumanda kuli padagu pamaso pace, Ndi kucionongeko kusowa cophimbako, |
| 7 |
| Ayala kumpoto popanda kanthu, Nalenjeka dziko pacabe. |
| 8 |
| Amanga madzi m'mitambo yace yocindikira; Ndi mtambo sung'ambika pansi pace, |
| 9 |
| Acingira pa mpando wace wacifumu, Nayalapo mtambo wace. |
| 10 |
| Analembera madziwo malire, Mpaka polekeza kuunika ndi mdima. |
| 11 |
| Mizati ya thambo injenjemera, Ndi kudabwa pa kudzudzula kwace. |
| 12 |
| Mwa mphamvu yace agwetsa nyanja bata; Ndipo mwa luntha lace akantha kudzikuza kwace. |
| 13 |
| Mwa mzimu wace anyezimiritsa thambo; Dzanja lace linapyoza njoka yothawayo. |
| 14 |
| Taonani, awa ndi malekezero a njira zace; Ndi cimene tikumva za Iye ndi cinong'onezo cacing'ono; Koma kugunda kwa mphamvu yace akuzindikiritsa ndani? |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/job/026.mp3
42
26