×

Buku Loyera

YOBU 26

1
Tsono Yobe adayankha kuti,
2
“Iwe, kodi wandithandiza ine munthu wosauka ndi wofookane ngati?
3
Kodi wandilangiza zabwino ine, munthu wopanda nzerune ngati? Kodi wandiwuza nzeru zambiri pamenepa ngati?
4
Kodi ndani adzamva mau akoŵa? Nanga udazitenga kuti zonsezi?
5
“Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa nthaka, zonse zokhala m'madzi pansipo zikuvutika.
6
Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu, ndipo kumeneko sikuphimbika kwa Iye.
7
Mulungu adayala thambo lakumpoto pa phompho, adakoloŵeka dziko lapansi m'malo mwake, pamene panali popanda nkanthu komwe.
8
Amasunga madzi ambiri m'mitambo yochindikira, koma mitamboyo sing'ambika.
9
Amaphimba mwezi, amauphimba ndi mtambo wake.
10
Madzi Mulungu adaŵalembera malire onga uta, motero adalekanitsa kuŵala ndi mdima.
11
Mizati yochirikiza thambo lakumwamba imanjenjemera ndi mantha, imazizwa pakumva kudzudzula kwa Mulungu.
12
Ndi mphamvu zake adatontholetsa nyanja, ndi nzeru zake adakantha chilombo cham'madzi chija cha Rahabu.
13
Ndi mpweya mwake adayeretsa zamumlengalenga, ndi dzanja lake adapha chinjoka chothaŵa chija.
14
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba