|
| 1 |
|
| Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wace, nati, |
|
| 2 |
|
| Ha! ndikadakhala monga m'miyezi yapitayi, Monga m'masiku akundisunga Mulungu; |
|
| 3 |
|
| Muja nyali yace inawala pamutu panga, Ndipo ndi kuunika kwace ndinayenda mumdima; |
|
| 4 |
|
| Monga umo ndinakhala m'masiku anga olimba, Muja uphungu wa Mulungu unakhala pahema panga; |
|
| 5 |
|
| Muja Wamphamvuyonse akali nane pamodzi, Ndi ana anga anandizinga; |
|
| 6 |
|
| Muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka, Ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta aazitona! |
|
| 7 |
|
| Muja ndinaturuka kumka kucipata kumudzi, Muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala, |
|
| 8 |
|
| Anyamata anandiona nabisala, Okalamba anandinyamukira, nakhala ciriri, |
|
| 9 |
|
| Akalonga anadziletsa kulankhula, Ndi kugwira pakamwa pao; |
|
| 10 |
|
| Mau a omveka anali zi, Ndi lilime lao linamamatira ku malakalaka ao. |
|
| 11 |
|
| Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa; Ndipo pondiona diso, linandicitira umboni. |
|
| 12 |
|
| Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakupfuula; Mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi. |
|
| 13 |
|
| Dalitso la iye akati atayike linandidzera, Ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauyimbitsa mokondwera. |
|
| 14 |
|
| Ndinabvala cilungamo, ndipo cinandibvala ine; Ciweruzo canga cinanga mwinjiro ndi nduwira. |
|
| 15 |
|
| Ndinali maso a akhungu, Ndi mapazi a otsimphina. |
|
| 16 |
|
| Ndinali atate wa waumphawi; Ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwa ndinafunsitsa. |
|
| 17 |
|
| Ndipo ndinatyola nsagwada ya wosalungama, Ndi kukwatula cogwidwa kumano kwace. |
|
| 18 |
|
| Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m'cisa canga; Ndipo ndidzacurukitsa masiku anga ngati mcenga. |
|
| 19 |
|
| Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi; Ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse. |
|
| 20 |
|
| Ulemu wanga udzakhala wosaguga mwa ine, Ndi uta wanga udzakhala wosalifuka m'dzanja mwanga. |
|
| 21 |
|
| Anthu anandimvera, nalindira, Nakhala cete, kuti ndiwapangire. |
|
| 22 |
|
| Nditanena mau anga sanalankhulanso, Ndi kunena kwanga kunawakhera. |
|
| 23 |
|
| Anandilindira ngati kulindira mvula, Nayasama pakamwa pao ngati kulira mvula ya masika. |
|
| 24 |
|
| Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima; Ndipo sanagwetsa kusangalala kwa nkhope yanga. |
|
| 25 |
|
| Ndinawasankhira njira yao ndi kukhala mkuru wao. Ndinakhala ngati mfumu mwa ankhondo ace, Ngati wotonthoza ofedwa. |
|
|
|
|