|
| 1 |
|
| Pambuyo pake Yobu anatsekula pakamwa pake nayamba kutemberera tsiku limene iyeyo anabadwa. |
|
| 2 |
|
| Ndipo Yobu anati: |
|
| 3 |
|
| “Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwe ndi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’ |
|
| 4 |
|
| Tsiku limenelo lisanduke mdima; Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso; kuwala kusaonekenso pa tsikulo. |
|
| 5 |
|
| Mdima ndi mthunzi wa imfa zikhale pa tsiku limeneli; mtambo uphimbe tsikuli; mdima wandiweyani udetse kuwala kwake. |
|
| 6 |
|
| Usiku umenewo ukutidwe ndi mdima wandiweyani; usawerengedwenso pamodzi ndi masiku a chaka, kapena kukhala pa mwezi wina uliwonse. |
|
| 7 |
|
| Usiku umenewo usabweretse chilichonse chabwino; kusamvekenso nthungululu za chikondwerero. |
|
| 8 |
|
| Odziwa kutemberera masiku alitemberere tsikulo, iwo amene akonzekera kuwutsa Leviyatani. |
|
| 9 |
|
| Nyenyezi zake za mʼbandakucha zikhale mdima; tsikulo liyembekezere kucha pachabe ndipo lisaonenso kuwala koyamba kwa mʼbandakucha. |
|
| 10 |
|
| Pakuti tsiku limenelo ndiye ndinatuluka mʼmimba ya amayi anga ndipo ndi limene linandionetsa zovuta. |
|
| 11 |
|
| “Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwa ndi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba? |
|
| 12 |
|
| Chifukwa chiyani panali mawondo wondilandirirapo ndi mawere woti andiyamwitsepo? |
|
| 13 |
|
| Pakuti tsopano bwenzi ndili gone mwamtendere; ndikanakhala nditagona tulo ndili pa mpumulo |
|
| 14 |
|
| pamodzi ndi mafumu ndi aphungu a dziko lapansi, amene anadzimangira nyumba zikuluzikulu zimene tsopano ndi mabwinja, |
|
| 15 |
|
| pamodzi ndi olamulira amene anali ndi golide, amene anadzaza nyumba zawo ndi siliva. |
|
| 16 |
|
| Kapena, bwanji sindinakwiriridwe pansi monga mwana wobadwa wakufa kale, ngati khanda limene silinaone kuwala kwa dzuwa? |
|
| 17 |
|
| Ku mandako anthu oyipa sakhalanso pa mavuto, ndipo kumeneko anthu otopa ali pa mpumulo. |
|
| 18 |
|
| A mʼndende kumeneko akusangalala ndi mtendere; sakumvanso mawu ofuwula a kapitawo wa akapolo. |
|
| 19 |
|
| Anthu wamba ndi anthu apamwamba ali kumeneko, ndipo kapolo ndi womasuka kwa mbuye wake. |
|
| 20 |
|
| “Chifukwa chiyani dzuwa limawalira iwo amene ali pa mavuto, ndipo moyo umapatsidwa kwa owawidwa mtima, |
|
| 21 |
|
| kwa iwo amene amalakalaka imfa imene sibwera, amene amayifunafuna imfayo kupambana chuma chobisika, |
|
| 22 |
|
| amene amakondwa ndi kusangalala akamalowa mʼmanda? |
|
| 23 |
|
| Chifuwa chiyani moyo umaperekedwa kwa munthu amene njira yake yabisika, amene Mulungu wamuzinga ponseponse? |
|
| 24 |
|
| Mʼmalo moti ndidye, ndimalira, ndi kubuwula kwanga nʼkosalekeza. |
|
| 25 |
|
| Chimene ndinkachiopa chandigwera; chimene ndinkachita nacho mantha chandichitikira. |
|
| 26 |
|
| Ndilibe mtendere kapena bata, ndilibe mpumulo, koma mavuto okhaokha.” |
|
|
|
|