|
| 1 |
|
| Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka, Iwo amene atate ao ndikadawapeputsa, osawaika pamodzi ndi agaru olinda nkhosa zanga. |
|
| 2 |
|
| Mphamvunso ya m'manja mwao ndikadapindulanji nayo? Ndiwo anthu amene unyamata wao udatha, |
|
| 3 |
|
| Atsala mafupa okha okha ndi kusowa ndi njala; Akungudza nthaka youma kuli mdima wa m'cipululu copasuka. |
|
| 4 |
|
| Achera terere lokolera kuzitsamba, Ndi cakudya cao ndico mizu ya dinde. |
|
| 5 |
|
| Anawapitikitsa pakati pa anthu, Awapfuulira ngati kutsata mbala. |
|
| 6 |
|
| Azikhala m'zigwa za cizirezire, M'maenje a m'nthaka ndi m'mapanga. |
|
| 7 |
|
| Pakati pa zitsamba alira ngati buru, Pansi pa khwisa asonkhana pamodzi. |
|
| 8 |
|
| Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina; Anawaingitsa kuwacotsa m'dziko. |
|
| 9 |
|
| Koma tsopano ndasanduka nyimbo ya oterewo, Nandiyesa nthanthi. |
|
| 10 |
|
| Anyansidwa nane, akhala patali ndi ine, Saleka kuthira malobvu pankhope panga. |
|
| 11 |
|
| Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza; Anataya comangira m'kamwa mwao pamaso panga. |
|
| 12 |
|
| Ku dzanja langa lamanja anauka oluluka, Akankha mapazi anga, Andiundira njira zao zakundiononga. |
|
| 13 |
|
| Aipsa njira yanga, Athandizana ndi tsoka langa; Ndiwo anthu omwewo osowa mthandizi. |
|
| 14 |
|
| Akudza ngati opitira pogamuka linga papakuru, Pakati pa zopasuka adzigubuduza kundidzera ine. |
|
| 15 |
|
| Anditembenuzira zondiopsa, Auluza ulemu wanga ngati mphepo; Ndi zosungika zanga zapita ngati mtambo. |
|
| 16 |
|
| Ndipo tsopano moyo wanga udzitsanulira m'kati mwanga; Masiku akuzunza andigwira. |
|
| 17 |
|
| Nyengo ya usiku mafupa anga awaza mwa ine, Ndi zowawa zondikungudza sizipuma. |
|
| 18 |
|
| Mwa mphamvu yaikuru ya nthenda yanga cobvala canga cinasandulika, Cindithina ngati pakhosi pa maraya anga. |
|
| 19 |
|
| Iye anandiponya m'matope, Ndipo ndafanana ndi pfumbi ndi phulusa. |
|
| 20 |
|
| Ndipfuula kwa Inu, koma simundiyankha; Ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera. |
|
| 21 |
|
| Mwasandulika kundicitira nkharwe; Ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza. |
|
| 22 |
|
| Mundikweza kumphepo, mundiyendetsa pomwepo; Ndipo mundisungunula mumkuntho. |
|
| 23 |
|
| Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa, Ndi ku nyumba yokomanamo amoyo onse. |
|
| 24 |
|
| Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lace kodi? Akati aonongeke, sapfuulako kodi? |
|
| 25 |
|
| Kodi sindinamlirira misozi wakulawa zowawa? Kodi moyo wanga sunacitira cisoni osowa? |
|
| 26 |
|
| Muja ndinayembekeza cokoma cinadza coipa, Ndipo polindira kuunika unadza mdima. |
|
| 27 |
|
| M'kati mwanga mupweteka mosapuma, Masiku a mazunzo andidzera. |
|
| 28 |
|
| Ndiyenda ndiri wothimbirira osati ndi dzuwa ai; Ndinyamuka mumsonkhano ndi kupfuula, |
|
| 29 |
|
| Ndiri mbale wao wa ankhandwe, Ndi mnansi wao wa nthiwatiwa. |
|
| 30 |
|
| Khungu langa lada, nilindipfundukira; Ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao. |
|
| 31 |
|
| Cifukwa cace zeze wanga wasandulika wa maliro, Ndi citoliro canga ca mau a olira misozi. |
|
|
|
|