|
| 1 |
|
| “Koma tsopano akundinyoza, ana angʼonoangʼono kwa ine, anthu amene makolo awo sindikanawalola kuti azithandizana ndi agalu anga kuweta nkhosa zanga. |
|
| 2 |
|
| Kodi mphamvu zawo ndi za phindu lanji kwa ine, pakuti mphamvu zawo zinatha kale? |
|
| 3 |
|
| Anali atatheratu kuwonda ndi njala, ankayendayenda mʼdziko lopanda madzi, mʼchipululu usiku. |
|
| 4 |
|
| Ankathyola therere ndi masamba owawa, ndipo chakudya chawo chinali mizu ya mitengo ya masache. |
|
| 5 |
|
| Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo, akuwakuwiza ngati kuti anali akuba. |
|
| 6 |
|
| Anawumirizidwa kukhala ku zigwembe za mitsinje yowuma, pakati pa matanthwe ndi mʼmaenje a mʼnthaka. |
|
| 7 |
|
| Ankalira ngati nyama kuthengo ndipo ankawunjikana pamodzi pa ziyangoyango. |
|
| 8 |
|
| Anali anthu achabechabe ndi wopanda dzina, anathamangitsidwa mʼdziko. |
|
| 9 |
|
| “Ndipo tsopano ana awo akundiyimba nyimbo zachipongwe; ineyo ndasanduka chisudzo chawo. |
|
| 10 |
|
| Iwo amanyansidwa nane ndipo amandithawa; akandiona salephera kundilavulira mʼmaso mwangamu. |
|
| 11 |
|
| Tsopano pakuti Mulungu wakhwefula uta wanga ndipo wandisautsa, iwowo analekeratu kundiopa. |
|
| 12 |
|
| Ku dzanja langa lamanja anthu akulimbana nane; andikumbira dzenje loti ndigweremo ndikamayenda, andipangira mitumbira ya nkhondo kuti alimbane nane. |
|
| 13 |
|
| Iwo anditsekera njira; akufuna kundichititsa ngozi, popanda wina aliyense wowaletsa. |
|
| 14 |
|
| Akundithamangitsa ngati madzi olowera pa mpanda wobowoka, iwo akubwererabwerera pakati pa chipasupasu. |
|
| 15 |
|
| Zoopsa zandithetsa mphamvu; ulemu wanga wachita ngati wauluzika ndi mphepo, chuma changa chija chazimirira ngati mtambo. |
|
| 16 |
|
| “Ndipo tsopano mtima wanga wachokamo; ndili mʼmasiku amasautso. |
|
| 17 |
|
| Mafupa anga akuphwanya usiku pakuti zowawa zanga sizikuleka. |
|
| 18 |
|
| Mʼmphamvu zake Mulungu wakhala ngati chovala changa; Iye wandigwira ngati chovala chondithina pa khosi. |
|
| 19 |
|
| Wandiponya mʼmatope, ndipo ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa. |
|
| 20 |
|
| “Inu Mulungu, ine ndikulirira kwa Inu, koma simukundiyankha; ndikayimirira, Inu simundiyangʼana nʼkomwe. |
|
| 21 |
|
| Inuyo mumandichitira zankhanza; mumandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu. |
|
| 22 |
|
| Mwandinyamulira ku mphepo ndipo mwandiwulutsa ndi mphepoyo; mwandiponya mʼmphepo ya mkuntho. |
|
| 23 |
|
| Ndikudziwa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa, kumalo kumene amoyo onse adzapitako. |
|
| 24 |
|
| “Ndithudi palibe munthu amene amalanga munthu wosweka mtima, amene akupempha thandizo mʼmasautso ake. |
|
| 25 |
|
| Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto? Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka? |
|
| 26 |
|
| Koma pamene ndinkayembekezera zabwino, zoyipa ndiye zinandigwera; pamene ndinkafunafuna kuwala, mdima ndiye unandigwera. |
|
| 27 |
|
| Kuwawa kwa mʼkati mwanga sikukuleka; ndili mʼmasiku amasautso. |
|
| 28 |
|
| Ndikuyenda wothimbirira, komatu osati ndi dzuwa; ndimayimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira. |
|
| 29 |
|
| Ndasanduka mʼbale wa nkhandwe, mnzawo wa akadzidzi. |
|
| 30 |
|
| Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka; thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi. |
|
| 31 |
|
| Pangwe wanga wasanduka woyimbira maliro, ndipo chitoliro changa chikuyimbira anthu olira. |
|
|
|
|