|
| 1 |
|
| Ndinapangana ndi maso anga, Potero ndipenyerenji namwali? |
|
| 2 |
|
| Pakuti gawo la Mulungu locokera kumwamba, Ndi colowa ca Wamphamvuyonse cocokera m'mwambamo nciani? |
|
| 3 |
|
| Si ndizo cionongeko ca wosalungama, Ndi tsoka la ocita mphulupulu? |
|
| 4 |
|
| Nanga sapenyanjira zanga, Ndi kuwerenga moponda mwanga monse? |
|
| 5 |
|
| Ngati ndinayanjana nalo bodza, Ndi phazi langa linathamangira cinyengo; |
|
| 6 |
|
| Andiyese ndi muyeso wolingana, Kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga. |
|
| 7 |
|
| Ngati phazi langa linapambuka m'njira, Ndi mtima wanga unatsata maso anga? Ngati cirema camamatira manja anga? |
|
| 8 |
|
| Ndibzale ine nadye wina, Ndi zondimerera ine zizulidwe. |
|
| 9 |
|
| Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi, Ngati ndalalira pa khomo la mnzanga, |
|
| 10 |
|
| Mkazi wanga aperere wina; Wina namuike kumbuyo. |
|
| 11 |
|
| Pakuti ico ndi coipitsitsa, Ndico mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wace. |
|
| 12 |
|
| Pakuti ndico moto wakunyeka mpaka cionongeko, Ndi cakuzula zipatso zanga zonse. |
|
| 13 |
|
| Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga, kapena wa mdzakazi wanga, Potsutsana nane iwo, |
|
| 14 |
|
| Ndidzatani ponyamuka Mulungu? Ndipo pondizonda Iye ndidzamyankha ciani? |
|
| 15 |
|
| Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenga iyenso? Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba? |
|
| 16 |
|
| Ngati ndakaniza aumphawi cifuniro cao, Kapena kutopetsa maso a amasiye, |
|
| 17 |
|
| Kapena kudya nthongo yanga ndekha, Osadyako mwana wamasiye; |
|
| 18 |
|
| (Pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa ndi ine monga ndi atate; Ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye cibadwire ine.) |
|
| 19 |
|
| Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda cobvala, Kapena kuti wosowa alibe copfunda; |
|
| 20 |
|
| Ngati zuuno zace sizinandiyamika, Ngati sanapfunda ubweya wa nkhosa zanga; |
|
| 21 |
|
| Ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa, Popeza ndinaona thandizo langa kucipata; |
|
| 22 |
|
| Libanthuke phewa langa paphalo, Ndi dzanja langa liduke pagwangwa. |
|
| 23 |
|
| Pakuti tsoka locokera kwa Mulungu linandiopsa, Ndi cifukwa ca ukulu wace sindinakhoza kanthu, |
|
| 24 |
|
| Ngati ndayesa golidi ciyembekezo canga, Ndi kunena ndi golidi woyengetsa, Ndiwe cikhazikitso canga; |
|
| 25 |
|
| Ngati ndinakondwera popeza cuma canga ncacikuru, Ndi dzanja langa lapeza zocuruka; |
|
| 26 |
|
| Ngati ndalambira dzuwa lirikuwala, Kapena mwezi ulikuyenda monyezimira; |
|
| 27 |
|
| Ndi mtima wanga wakopeka m'tseri, Ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa; |
|
| 28 |
|
| Icinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wace; Pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba. |
|
| 29 |
|
| Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida, Kapena kudzitukula pompeza coipa; |
|
| 30 |
|
| Ndithu sindinalola m'kamwa mwanga mucimwe, Kupempha motemberera moyo wace. |
|
| 31 |
|
| Ngati amuna a m'hema mwanga sanati, Ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu? |
|
| 32 |
|
| Mlendo sakagona pakhwalala, Koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga. |
|
| 33 |
|
| Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu, Ndi kubisa mphulupulu yanga m'cifuwa mwanga; |
|
| 34 |
|
| Popeza ndinaopa unyinji waukuru, Ndi cipepulo ca mapfuko cinandiopsetsa; Potero ndinakhala cete osaturuka pakhomo panga. |
|
| 35 |
|
| Ha! ndikadakhala naye wina wakundimvera, Cizindikilo canga sici, Wamphamvuyonse andiyankhe; Mwenzi ntakhala nao mau akundineneza analemberawo mdani wangal |
|
| 36 |
|
| Ndithu ndikadawasenza paphewa panga, Ndi kudzimangirira awa ngati korona. |
|
| 37 |
|
| Ndikadamfotokozera ciwerengo ca mopondamo mwanga, Ndikadamsenderera Iye ngati ka longa, |
|
| 38 |
|
| Ngati minda yanga ipfuula monditsutsa, Ndi nthumbira zace zilira pamodzi; |
|
| 39 |
|
| Ngati ndadya zipatso zace wopanda ndarama, Kapena kutayitsa eni ace moyo wao; |
|
| 40 |
|
| Imere minga m'malo mwa tirigu, Ndi dawi m'malo mwa barele. Mau a Yobu atha. |
|
|
|
|