|
| 1 |
|
| “Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga; mutcherere khutu zonse zimene ndinene. |
|
| 2 |
|
| Tsopano ndiyamba kuyankhula; mawu anga ali pa msonga ya lilime langa. |
|
| 3 |
|
| Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama; pakamwa panga pakuyankhula zoonadi zimene ndikuzidziwa. |
|
| 4 |
|
| Mzimu wa Mulungu wandiwumba, mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo. |
|
| 5 |
|
| Mundiyankhe ngati mungathe; konzekani tsopano kuti munditsutse. |
|
| 6 |
|
| Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu; nanenso ndinachokera ku dothi. |
|
| 7 |
|
| Musachite mantha ndipo musandiope ayi, Ine sindikupanikizani kwambiri ayi. |
|
| 8 |
|
| “Koma inu mwayankhula ine ndikumva, ndamva mawu anuwo onena kuti, |
|
| 9 |
|
| ‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo; ndine woyera mtima ndipo ndilibe cholakwa. |
|
| 10 |
|
| Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo; Iye akundiyesa ngati mdani wake. |
|
| 11 |
|
| Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo, akulonda mayendedwe anga onse.’ |
|
| 12 |
|
| “Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi, pakuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu. |
|
| 13 |
|
| Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iye kuti sayankha mawu ena aliwonse a munthu? |
|
| 14 |
|
| Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana, ngakhale munthu sazindikira zimenezi. |
|
| 15 |
|
| Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku, pamene anthu ali mʼtulo tofa nato pamene akungosinza chabe pa bedi, |
|
| 16 |
|
| amawanongʼoneza mʼmakutu ndi kuwaopseza ndi machenjezo ake, |
|
| 17 |
|
| kumuchotsa munthu ku zoyipa, ndi kuthetseratu kunyada kwake, |
|
| 18 |
|
| kumulanditsa munthu ku manda, kuti moyo wake usawonongeke ndi lupanga. |
|
| 19 |
|
| “Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake, nthawiyo thupi lake lonse limangophwanya, |
|
| 20 |
|
| kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya, ndipo amanyansidwa ndi chakudya chabwino chomwe. |
|
| 21 |
|
| Thupi lake limawonda ndipo mafupa ake, omwe anali obisika, tsopano amaonekera poyera. |
|
| 22 |
|
| Munthuyo amayandikira ku manda, moyo wake umayandikira kwa amene amabweretsa imfa. |
|
| 23 |
|
| “Koma patakhala mngelo ngati mthandizi, mmodzi mwa ambirimbiri oterewa, adzafotokoza zimene zili zoyenera, |
|
| 24 |
|
| kudzamukomera mtima ndi kunena kuti, ‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda; ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’ |
|
| 25 |
|
| pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana; ndipo adzabwezeretsedwanso kukhala ngati mʼmasiku a unyamata wake. |
|
| 26 |
|
| Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa. Mulungu adzamulandira mwa chimwemwe ndipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba. |
|
| 27 |
|
| Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti, ‘Ndinachimwa ndipo sindinachite zolungama, koma sindinalangidwe koyenerana ndi kuchimwa kwanga. |
|
| 28 |
|
| Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda, ndipo ndidzakhala ndi moyo ndi kuonanso kuwala kwa dzuwa.’ |
|
| 29 |
|
| “Mulungu amachita zonsezi kwa munthu kawirikawiri, |
|
| 30 |
|
| kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda, kuti athe kuonanso kuwala kwa moyo. |
|
| 31 |
|
| “Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere; khalani chete kuti ndiyankhule. |
|
| 32 |
|
| Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni; yankhulani, pakuti ine ndikufuna mupezeke wolungama. |
|
| 33 |
|
| Koma ngati sichoncho, mundimvere; khalani chete ndipo ine ndidzakuphunzitsani nzeru.” |
|
|
|
|