|
| 1 |
|
| “Koma tsopano inu aYobe, mverani mau anga, mutchere khutu ku zonse zimene ndinene. |
|
| 2 |
|
| Tsopano ndiyamba kulankhula, ndikuuzani za mumtima mwanga. |
|
| 3 |
|
| Mau anga akusonyeza kulungama kwa mtima wanga, zimene ndimazidziŵa ndimalankhula moona. |
|
| 4 |
|
| Mzimu wa Mulungu udandiwumba. Mpweya wa Mphambe udandipatsa moyo. |
|
| 5 |
|
| Mundiyankhe ngati mungathe. Mulankhule mau anu tsatanetsatane pamaso panga, konzekani tsono. |
|
| 6 |
|
| Kunena zoona, ine ndine mnzanu pamaso pa Mulungu, poti inenso adandiwumba ndi dothi. |
|
| 7 |
|
| Musachite mantha ndi kuwopsedwa nane, chifukwa sindikupanikizani koopsa ai. |
|
| 8 |
|
| “Zoonadi, ndamva zimene mwalankhula, mau anu ndaŵatsata bwino. |
|
| 9 |
|
| Inu mukuti, ‘Ndine woyera mtima, ndilibe cholakwa. Ndine wolungama, ndilibe tchimo. |
|
| 10 |
|
| Mulungu wandipeza zifukwa zoti anditsutse nazo, Iye akundiyesa mdani wake. |
|
| 11 |
|
| Akumanga mapazi anga m'zigologolo, akulonda mayendedwe anga onse.’ |
|
| 12 |
|
| “Inu aYobe simukukhoza pa zimenezi, popeza kuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu. |
|
| 13 |
|
| Chifukwa chiyani mukulimbana ndi Mulungu nkumanena kuti, ‘Pa mau angaŵa sadzayankhapo ndi amodzi omwe?’ |
|
| 14 |
|
| Pajatu Mulungu amalankhula mwa njira zosiyanasiyana, koma anthu sazindikira zimenezo. |
|
| 15 |
|
| M'maloto, m'masomphenya usiku, pamene anthu ali m'tulo tofa nato, pamene akungosinza chabe pa bedi, |
|
| 16 |
|
| pamenepo amaŵatsekula makutu anthuwo, naŵaopsa ndi machenjezo. |
|
| 17 |
|
| Mulungu amachita izi kuti amletse munthu zoipa zimene amachita, amafuna kuthetseratu kunyada kwake. |
|
| 18 |
|
| Amalanditsa munthu ku manda, amapulumutsa moyo wake kuti ungaonongeke ndi lupanga. |
|
| 19 |
|
| “Mwina Mulungu amalanganso munthu ndi matenda kuti akonzeke, nthaŵiyo thupi lake lonse limangophwanya. |
|
| 20 |
|
| Choncho moyo wake umanyansidwa ndi chakudya chomwe, sangadye ngakhale zakudya zabwino. |
|
| 21 |
|
| Thupi lake limaonda, osatha kulithira m'maso, ndipo mafupa ake amene kale sankaoneka, amaonekera poyera. |
|
| 22 |
|
| Munthuyo akutsikira ku manda, ali pafupi kupita ku malo a anthu akufa. |
|
| 23 |
|
| Koma pataoneka mngelo, ngati mthandizi, mmodzi mwa ambirimbiri otere, wodzamkumbutsa zimene zili zoyenera, |
|
| 24 |
|
| ngati mngeloyo amkomera mtima, nati, ‘Mpulumutseni kuti asapite ku manda, dipo lake nali,’ |
|
| 25 |
|
| pamenepo thupi lake lisanduke lasee ngati lapaubwana, ndipo iye abwerere ku masiku a unyamata wake, |
|
| 26 |
|
| Tsono munthu amapemphera kwa Mulungu, Iyeyo nkumulandira. Amabwera pamaso pa Mulungu mokondwa, ndipo Mulungu amamchitira zolungama. |
|
| 27 |
|
| Apo adzavomera pamaso pa anthu kuti, ‘Ndidachimwa, sindidachite zolungama. Koma Mulungu sadandilange koyenerana ndi kuchimwa kwanga. |
|
| 28 |
|
| Iye adandipulumutsa kuti ndisapite ku manda, ndidzaonanso kuŵala kwa dzuŵa!’ |
|
| 29 |
|
| “Zoonadi, Mulungu amachita zonsezi kaŵirikaŵiri ndi anthu. |
|
| 30 |
|
| Amapulumutsa moyo wa munthu ku malo a imfa, kuti athe kuwonanso kuŵala kwa moyo. |
|
| 31 |
|
| “Inu aYobe, mutchere khutu, mundimvere ine. Mukhale chete, kuti ine ndilankhule. |
|
| 32 |
|
| Ngati muli ndi mau, mundiyankhe. Mulankhule, chifukwa ndifuna kuti mupezeke wolungama. |
|
| 33 |
|
| Ngati si choncho, mumvere ine, khalani chete, ndipo ine ndikuphunzitsani nzeru.” Mulungu ndiyedi wolungama. |
|
|
|
|