Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti, |
| 2 |
| “Kodi mukuganiza kuti mukukhoza? Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’ |
| 3 |
| Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani, ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’ |
| 4 |
| “Ine ndikufuna ndikuyankheni inu pamodzi ndi abwenzi anu omwe. |
| 5 |
| Yangʼanani kumwamba ndipo muone mitambo imene ili kutali ndi inuyo. |
| 6 |
| Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani? Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye? |
| 7 |
| Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani? Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu? |
| 8 |
| Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo, ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu. |
| 9 |
| “Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa; akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu. |
| 10 |
| Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga, amene amatisangalatsa nthawi ya usiku, |
| 11 |
| amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’ |
| 12 |
| Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa. |
| 13 |
| Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake; Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi. |
| 14 |
| Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti Iye saona zimene zikuchitika. Iye adzaweruza molungama ngati inu mutamudikira |
| 15 |
| ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango, zoyipa zambiri zimene anthu amachita, |
| 16 |
| abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake, mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.” |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/job/035.mp3
42
35