|
| 1 |
|
| Elihu nabwereza, nati, |
|
| 2 |
|
| Mundilole pang'ono, ndidzakuuzani, Pakuti ndiri naonso mau akunenera Mulungu. |
|
| 3 |
|
| Ndidzatenga nzeru zanga kutali, Ndidzabvomereza kuti Mlengi wanga ndi wolungama. |
|
| 4 |
|
| Pakuti zoonadi, mau anga sali abodza, Wakudziwitsa mwangwiro ali nanu. |
|
| 5 |
|
| Taonani, Mulungu ndiye mwini mphamvu, ndipo sapeputsa munthu; Mphamvu ya nzeru zace ndi yaikuru. |
|
| 6 |
|
| Sasunga woipa akhale ndi moyo, Koma awaninkha ozunzikazowayenera iwo. |
|
| 7 |
|
| Sawacotsera wolungama maso ace, Koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao Awakhazika cikhazikire, ndipo akwezeka. |
|
| 8 |
|
| Ndipo akamangidwa m'nsinga, Nakakodwa ndi zingwe za mazunzo, |
|
| 9 |
|
| Pamenepo awafotokozera nchito zao, Ndi zolakwa zao, kuti anacita modzikuza. |
|
| 10 |
|
| Awatseguliranso m'khutu mwao kuti awalangize, Nawauza abwerere kuleka mphulupulu. |
|
| 11 |
|
| Akamvera ndi kumtumikira, Adzatsiriza masiku ao modala, Ndi zaka zao mokondwera. |
|
| 12 |
|
| Koma akapanda kumvera adzatayika ndi lupanga, Nadzatsirizika osadziwa kanthu. |
|
| 13 |
|
| Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo, Akawamanga Iye, sapfuulira. |
|
| 14 |
|
| Iwowa akufa akali biriwiri, Ndi moyo wao utayika ngati odetsedwa. |
|
| 15 |
|
| Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwace, Nawatsegulira m'khutu mwao mwa kupsinjika kwao. |
|
| 16 |
|
| Inde akadakukopani mucoke posaukira, Mulowe kucitando kopanda copsinja; Ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu. |
|
| 17 |
|
| Koma mukadzazidwa nazo zolingirira oipa, Zolingirirazo ndi ciweruzo zidzakugwiranibe, |
|
| 18 |
|
| Pakuti mucenjere, mkwiyo ungakunyengeni mucite mnyozo; Ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli. |
|
| 19 |
|
| Cuma canu cidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika, Kapena mphamvu yanu yonse yolimba? |
|
| 20 |
|
| Musakhumbe usiku, Umene anthu alikhidwe m'malo mwao. |
|
| 21 |
|
| Cenjerani, musaluniike kumphulupulu; Pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa. |
|
| 22 |
|
| Taonani, Mulungu acita mokwezeka mu mphamvu yace, Mphunzitsi wakunga Iye ndani? |
|
| 23 |
|
| Anamuikira njira yace ndani? Adzati ndani, Mwacita cosalungama? |
|
| 24 |
|
| Kumbukilani kuti mukuze nchito zace, Zimene anaziyimbira anthu. |
|
| 25 |
|
| Anthu onse azipenyerera, Anthu aziyang'anira kutali. |
|
| 26 |
|
| Taonani, Mulungu ndiye wamkuru, ndipo sitimdziwa; Ciwerengo ca zaka zace ncosasanthulika. |
|
| 27 |
|
| Pakuti akweza madontho a mvula, Akhetsa mvula ya m'nkhungu yace |
|
| 28 |
|
| Imene mitambo itsanulira, Nibvumbitsira anthu mocuruka. |
|
| 29 |
|
| Pali munthu kodi wodziwitsa mayalidwe a mitambo, Ndi kugunda kwa msasa wace? |
|
| 30 |
|
| Taonani, Iye ayala kuunika kwace pamenepo. Nabvundikira kunsi kwace kwa nyanja. |
|
| 31 |
|
| Pakuti aweruza nazo mitundu ya anthu. Apatsa cakudya cocuruka. |
|
| 32 |
|
| Akutidwa manja ace ndi mphezi, Nailamulira igwere pofunapo Iye. |
|
| 33 |
|
| Kugunda kwace kulalikira za Iye, Zoweta zomwe zilota mtambo woyandikira. |
|
|
|
|