|
| 1 |
|
| Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati: |
|
| 2 |
|
| “Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsani kuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu. |
|
| 3 |
|
| Nzeru zanga ndimazitenga kutali; ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga. |
|
| 4 |
|
| Ndithudi mawu anga si abodza; wanzeru zangwiro ali ndi inu. |
|
| 5 |
|
| “Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu; Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake. |
|
| 6 |
|
| Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyo koma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa. |
|
| 7 |
|
| Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama; amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumu ndipo amawalemekeza mpaka muyaya. |
|
| 8 |
|
| Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo, ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso, |
|
| 9 |
|
| Iye amawafotokozera zomwe anachita, kuti iwo anachimwa modzikuza. |
|
| 10 |
|
| Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo ake ndipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo. |
|
| 11 |
|
| Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira, adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere, adzatsiriza zaka zawo mosangalala. |
|
| 12 |
|
| Koma ngati samvera, adzaphedwa ndi lupanga ndipo adzafa osadziwa kanthu. |
|
| 13 |
|
| “Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo; akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo. |
|
| 14 |
|
| Amafa akanali achinyamata, pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo. |
|
| 15 |
|
| Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo; Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo. |
|
| 16 |
|
| “Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso, kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani, kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri. |
|
| 17 |
|
| Koma tsopano inu mwapezeka wopalamula chifukwa cha kuyipa kwanu; chiweruzo ndi chilungamo chakugwerani. |
|
| 18 |
|
| Muchenjere kuti wina asakukopeni ndi chuma; musalole kuti chiphuphu chachikulu chikusocheretseni. |
|
| 19 |
|
| Kodi chuma chanu kapena mphamvu zanu zonse zingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso? |
|
| 20 |
|
| Musalakalake kuti usiku ubwere, pakuti ndiyo nthawi imene anthu adzawonongeka. |
|
| 21 |
|
| Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo, chifukwa uchimowo ndiwo unabweretsa kuzunzika kwanu. |
|
| 22 |
|
| “Taonani, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu. Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye? |
|
| 23 |
|
| Kodi ndani amene anamuwuzapo Mulungu zoti achite, kapena kumuwuza kuti, ‘Inu mwachita chinthu cholakwa?’ |
|
| 24 |
|
| Kumbukirani kutamanda ntchito zake zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo. |
|
| 25 |
|
| Anthu onse amaziona ntchitozo; anthuwo amaziona ali kutali. |
|
| 26 |
|
| Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu, sitimudziwa nʼpangʼono pomwe! Chiwerengero cha zaka zake nʼchosadziwika. |
|
| 27 |
|
| “Mulungu ndiye amakweza timadontho tamadzi kuthambo, timene timasungunuka nʼkukhala mvula; |
|
| 28 |
|
| mitambo imagwetsa mvulayo ndipo mvulayo imavumbwa pa anthu mokwanira. |
|
| 29 |
|
| Kodi ndani amene angadziwe momwe mitambo imayendera, momwe Iye amabangulira kuchokera kumalo ake? |
|
| 30 |
|
| Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse, zimafika ngakhale pansi pa nyanja. |
|
| 31 |
|
| Umu ndi mmene Iye amalamulira mitundu ya anthu ndi kuwapatsa chakudya chochuluka. |
|
| 32 |
|
| Amadzaza manja ake ndi zingʼaningʼani, ndipo amazilamulira kuti zigwe pamalo pamene Iye akufuna. |
|
| 33 |
|
| Mabingu ake amalengeza za kubwera kwa mvula yamkuntho; ngʼombe nazo zimalengeza za kubwera kwake. |
|
|
|
|