|
| 1 |
|
| Ndipo Elihu adapitirira kulankhula, nati: |
|
| 2 |
|
| “Mundilole pang'ono, ndipo ndikuphunzitsani. Pakuti zilipobe zoti ndinene m'malo mwa Mulungu. |
|
| 3 |
|
| Nzeru zanga zikhala zochokera patali, ndiwonetsa kulungama kwa Mlengi wanga. |
|
| 4 |
|
| Ndithudi, sindikunena zabodza. Wolankhula nanune ndine wanzeru kotheratu. |
|
| 5 |
|
| “Zoonadi, Mulungu ndi wamphamvu, sanyoza munthu aliyense, ndipo amadziŵa zonse. |
|
| 6 |
|
| Salola oipa kuti akhalebe ndi moyo, koma anthu osauka amaŵachitira zolungama. |
|
| 7 |
|
| Iyeyo amatchinjiriza anthu opanda chifukwa, amalola kuti alamulire ngati mafumu, ndipo motero amalemekezeka mpaka muyaya. |
|
| 8 |
|
| Koma anthu akamangidwa ndi nsinga, namazunzika chifukwa cha zimene adachita, |
|
| 9 |
|
| pamenepo Mulungu amaŵasonyeza ntchito zao ndi zolakwa zao, kutsutsa kudzikuza kwao kochita kunyanya. |
|
| 10 |
|
| Amaŵatsekula makutu kuti amve malangizo ake, amaŵalamula kuti asiye zoipa. |
|
| 11 |
|
| Ngati anthu amumvera ndi kumamtumikira, adzatsiriza masiku a moyo wao mwamtendere, adzatsiriza zaka zao mosangalala. |
|
| 12 |
|
| Koma akapanda kumvera, adzaonongeka ndi lupanga, adzafa osadziŵa kanthu. |
|
| 13 |
|
| “Anthu onyoza Mulungu mumtima mwao amaputa mkwiyo wake, Mulungu akaŵalanga, iwo safuula kupempha chithandizo. |
|
| 14 |
|
| Amafa akali biriŵiri, ndipo moyo wao umathera m'zonyansa. |
|
| 15 |
|
| Koma Mulungu amapulumutsa ovutika mwa njira ya mazunzo ao omwe, amaŵatsekula makutu poŵagwetsa m'mavuto. |
|
| 16 |
|
| Inuyo Mulungu adakutulutsaninso m'mavutowo, afuna kukuikani pabwino, osasoŵa kanthu kalikonse. |
|
| 17 |
|
| “Koma tsopano inu mwapezeka opalamula ngati anthu oipa, choncho chilango cholungama cha Mulungu chakugwerani. |
|
| 18 |
|
| Muchenjere kuti chuma chingakuphimbeni m'maso, musalole kuti chiphuphu chikusokezeni. |
|
| 19 |
|
| Kodi kulira kwanu kungakuchotseni m'mavuto? Kodi mphamvu zanu zingakupulumutseni? |
|
| 20 |
|
| Musalakelake kuti usiku ubwere, chifukwa ndiyo nthaŵi imene mitundu ya anthu idzaonongeka. |
|
| 21 |
|
| Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo, chifukwa uchimowu ndiwo udadzetsa kuzunzika kwanu. |
|
| 22 |
|
| Zoonadi, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu. Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye? |
|
| 23 |
|
| Palibe ndi mmodzi yemwe angauze Mulungu zoti achite. Palibe aliyense amene anganene kuti ‘Mulungu ndi wolakwa.’ |
|
| 24 |
|
| “Kumbukirani kutamanda ntchito za Mulungu, zimene anthu amaziyamika ndi nyimbo. |
|
| 25 |
|
| Anthu onse amaona ntchitozo, koma palibe wozindikira m'mene ziliri. |
|
| 26 |
|
| Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu kwambiri, sitimdziŵa mpang'ono pomwe. Chiŵerengero cha zaka zake nchosadziŵika. |
|
| 27 |
|
| Mulungu ndiye amakweza timadontho ta madzi ku thambo kuchokera pansi, ndipo amasungunula mitambo kuti ikhale mvula. |
|
| 28 |
|
| Mitambo imatsanyula mvulayo, ndipo mvulayo imavumba pa anthu mokwanira. |
|
| 29 |
|
| Kodi alipo wina woti angadziŵe kuyenda kwa mitambo kapena kugunda kwa zing'aning'ani? |
|
| 30 |
|
| Mulungu amaŵalitsa zing'aning'ani kuthambo kwake konse, zimafika ngakhale pansi pa nyanja. |
|
| 31 |
|
| Mulungu amachenjeza mitundu ya anthu podzera m'zimenezi, komabe amapereka chakudya chochuluka. |
|
| 32 |
|
| Amagwira zing'aning'ani, ndipo amazilamula kuti zigwe pa malo amene Iye akufuna. |
|
| 33 |
|
| Kugunda kwake kumalengeza kuti Iye alipo, ndiye amalanga uchimo mwaukali. |
|
|
|
|