|
| 1 |
|
| Pa icinso mtima wanga unienjemera, Nusunthika m'malo mwace. |
|
| 2 |
|
| Mvetsetsani cibumo ca mau ace, Ndi kugunda koturuka m'kamwa mwace. |
|
| 3 |
|
| Akumveketsa pansi pa thambo ponse, Nang'anipitsa mphezi yace ku malekezero a dziko lapansi. |
|
| 4 |
|
| Mau abuma kuitsata, Agunda ndi mau a ukulu wace, Ndipo sailetsa atamveka mau ace, |
|
| 5 |
|
| Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ace, Acita zazikuru osazidziwa ife. |
|
| 6 |
|
| Pakuti anena kwa cipale cofewa, Ugwe padziko. Momwemonso kwa mvula, Ndi kwa mbvumbi waukuru. |
|
| 7 |
|
| Atsekereza mokhomera cizindikilo dzanja la munthu ali yense, Kuti anthu onse anawalenga adziwe. |
|
| 8 |
|
| Pamenepo zirombo zilowa mobisalamo, Nizikhala m'ngaka mwao. |
|
| 9 |
|
| M'cipinda mwace muturuka kabvumvulu, Ndi cisanu cifuma kumpoto. |
|
| 10 |
|
| Mwa kupuma kwace apereka cipale, Ndi madzi acitando aundana. |
|
| 11 |
|
| Asenzetsanso mtambo wakuda bii madzi, Afunyulula mtambo wokhalamo mphezi yace; |
|
| 12 |
|
| Ndipo utembenuka-tembenuka pakulangiza kwace, Kuti ucite ziri zonse aulamulira, Pa nkhope ya dziko lokhalamo anthu; |
|
| 13 |
|
| Ngati aufikitsira dziko lace kulidzudzula, Kapena kulicitira cifundo. |
|
| 14 |
|
| Tamverani ici, Yobu. Taimani, mulingirire zodabwiza za Mulungu. |
|
| 15 |
|
| Kodi mudziwa umo Mulungu azilangizira zimenezi, Nawalitsa mphezi ya m'mtambo mwace? |
|
| 16 |
|
| Kodi mudziwa madendekeredwe ace a mitambo, Zodabwiza za Iye wakudziwa mwangwiro? |
|
| 17 |
|
| Kodi mudziwa umo zobvala zanu zifundira, Pamene dziko liri thuu cifukwa ca mwela? |
|
| 18 |
|
| Kodi muyala thambo pamodzi ndi Iye, Ndilo lolimba ngati kalirole woyengeka? |
|
| 19 |
|
| Mutilangize cimene tidzanena ndi Iye; Sitidziwa kulongosola mau athu cifukwa ca mdima. |
|
| 20 |
|
| Kodi munthu ayenera kumuuza kuti ndifuna kunena, Kapena kodi munthu adzakhumba kumezedwa? |
|
| 21 |
|
| Ndipo tsopano anthu sakhoza kupenyerera kuunika pakunyezimira kuthambo, Ndi mphepo yapita ndi kuuyeretsa, |
|
| 22 |
|
| Kucokera kumpoto kudzera kuwala konyezimira, Mulungu ali nao ukulu woopsa. |
|
| 23 |
|
| Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; Koma mwa ciweruzo ndi cilungamo cocuruka samasautsa. |
|
| 24 |
|
| M'mwemo anthu amuopa, Iye sasamalira ali yense wanzeru mumtima. |
|
|
|
|