|
| 1 |
|
| Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati: |
|
| 2 |
|
| “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga poyankhula mawu opanda nzeru? |
|
| 3 |
|
| Onetsa chamuna; ndikufunsa ndipo undiyankhe. |
|
| 4 |
|
| “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi? Ndiwuze ngati ukudziwa. |
|
| 5 |
|
| Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa! Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli? |
|
| 6 |
|
| Kodi maziko ake anawakumba potani, kapena ndani anayika mwala wake wapangodya, |
|
| 7 |
|
| pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa? |
|
| 8 |
|
| “Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa, pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko, |
|
| 9 |
|
| pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani, |
|
| 10 |
|
| pamene ndinayilembera malire ake ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake. |
|
| 11 |
|
| Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’ |
|
| 12 |
|
| “Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa, kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake, |
|
| 13 |
|
| kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi ndi kuthamangitsa anthu oyipa? |
|
| 14 |
|
| Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo; zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala. |
|
| 15 |
|
| Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa, ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu. |
|
| 16 |
|
| “Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja kapena pa magwero ake ozama? |
|
| 17 |
|
| Kodi anakuonetsapo zipata za imfa? Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani? |
|
| 18 |
|
| Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa? Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi. |
|
| 19 |
|
| “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti? Nanga mdima umakhala kuti? |
|
| 20 |
|
| Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi? Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko? |
|
| 21 |
|
| Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale! Wakhala ndi moyo zaka zambiridi! |
|
| 22 |
|
| “Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana kapena unayionapo nyumba yosungira matalala, |
|
| 23 |
|
| zimene ndazisungira nthawi ya mavuto ndi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo? |
|
| 24 |
|
| Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani kapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi? |
|
| 25 |
|
| Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula, nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi, |
|
| 26 |
|
| kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu, chipululu chopandamo munthu, |
|
| 27 |
|
| kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa ndi kumeretsamo udzu? |
|
| 28 |
|
| Kodi mvula ili ndi abambo ake? Nanga madzi a mame anawabereka ndani? |
|
| 29 |
|
| Kodi madzi owundana anawabereka ndani? Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba |
|
| 30 |
|
| pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala, pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa? |
|
| 31 |
|
| “Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi? Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana? |
|
| 32 |
|
| Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake kapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake? |
|
| 33 |
|
| Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa? Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi? |
|
| 34 |
|
| “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo kuti igwetse mvula ya chigumula? |
|
| 35 |
|
| Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime? Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’ |
|
| 36 |
|
| Kodi ndani anayika nzeru mu mtima, ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu? |
|
| 37 |
|
| Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo? Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo |
|
| 38 |
|
| pamene fumbi limasanduka matope, ndipo matopewo amawumbika? |
|
| 39 |
|
| “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi ndi kukhutitsa misona ya mikango |
|
| 40 |
|
| pamene ili khale mʼmapanga mwawo kapena pamene ikubisala pa tchire? |
|
| 41 |
|
| Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani pamene ana ake akulirira kwa Mulungu ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya? |
|
|
|
|