|
| 1 |
|
| Kodi udziwa nyengo yakuswana zinkhoma? Kodi wapenyerera pakuswa nswala? |
|
| 2 |
|
| Ukhoza kodi kuwerenga miyezi yakuzipitira, Kapena udziwa nyengo yoti ziswane? |
|
| 3 |
|
| Zithuntha, ziswa, Zitaya zowawa zao. |
|
| 4 |
|
| Ana ao akhala ojinca, akulira kuthengo, Acoka osabwerera kwa amao. |
|
| 5 |
|
| Ndani walola mbidzi ituruke yaufulu? Anaimasulira mbidzi nsinga zace ndani, |
|
| 6 |
|
| Imene ndaciyesa cipululu nyumba yace, Ndi dziko lakhulo pokhala pace? |
|
| 7 |
|
| Aseka phokoso la kumudzi, Osamva kukuwa kwa wofulumiza nyama za m'goli. |
|
| 8 |
|
| Poyenda ponse pamapiri mpa busa pace; Ilondola caciwisi ciri conse. |
|
| 9 |
|
| Kodi njati idzabvomera kukutumikira, Idzakhala ku codyetseramo cako kodi? |
|
| 10 |
|
| Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lace ilime m'mcera? Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m'zigwa? |
|
| 11 |
|
| Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yace njaikuru? Udzaisiyira nchito yako kodi? |
|
| 12 |
|
| Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako, Ndi kuzisonkhanitsira kudwale? |
|
| 13 |
|
| Phiko la nthiwatiwa likondwera, Koma mapiko ndi nthenga zace nzofatsa kodi? |
|
| 14 |
|
| Pakuti isiya mazira ace panthaka, Nimafunditsa m'pfumbi, |
|
| 15 |
|
| Niiwala kuti phazi lingawaphwanye, Kapena cirombo cingawapondereze. |
|
| 16 |
|
| Iumira mtima ana ace monga ngati sali ace; Idzilemetsa ndi nchito cabe, popeza iribe mantha; |
|
| 17 |
|
| Pakuti Mulungu anaimana nzeru, Ndipo sanaigawira luntha. |
|
| 18 |
|
| Ikafika nthawi yace, iweramuka, Iseka kavalo ndi wa pamsana pace. |
|
| 19 |
|
| Wampatsa kavalo mphamvu yace kodi? Wambveka pakhosi pace cenjerere cogwedezeka? |
|
| 20 |
|
| Wamlumphitsa kodi ngati dzombe? Ulemerero wa kumina kwace ngwoopsa. |
|
| 21 |
|
| Apalasa kucigwa, nakondwera nayo mphamvu yace; Aturuka kukomana nao eni zida. |
|
| 22 |
|
| Aseka mantha osaopsedwa, Osabwerera kuthawa lupanga. |
|
| 23 |
|
| Phodo likuti koco koco panthiti pace, Mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe. |
|
| 24 |
|
| Ndi kunjenjemera kwaukali aimeza nthaka, Osaimitsika pomveka lipenga. |
|
| 25 |
|
| Pomveka lipenga akuti, Hee! Anunkhiza nkhondo irikudza kutali Kugunda kwa akazembe ndi kuhahaza, |
|
| 26 |
|
| Kodi kabawi auluka mwa nzeru zako, Natambasula mapiko ace kumka kumwera? |
|
| 27 |
|
| Kodi ciombankhanga cikwera m'mwamba pocilamulira iwe, Nicimanga cisanja cace m'mwamba? |
|
| 28 |
|
| Kwao nku thanthwe, cigona komweko, Pansonga pa thanthwe pokhazikikapo. |
|
| 29 |
|
| Pokhala kumeneko ciyang'ana cakudya; Maso ace acipenyetsetsa ciri kutali, |
|
| 30 |
|
| Ana ace akumwa mwazi, Ndipo pomwe pali ophedwa, apo pali ico. |
|
|
|
|