|
| 1 |
|
| Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti, |
|
| 2 |
|
| “Ngati wina atakuyankha, kodi ungakhumudwe? Koma ndani angakhale chete wosayankhula? |
|
| 3 |
|
| Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri, momwe walimbitsira anthu ofowoka. |
|
| 4 |
|
| Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa; unachirikiza anthu wotha mphamvu. |
|
| 5 |
|
| Koma tsopano mavuto akufikira ndipo wataya mtima, zakukhudza ndipo uli ndi mantha. |
|
| 6 |
|
| Kodi kuopa Mulungu kwako sindiko kulimbika mtima kwako? Ndipo moyo wako wosalakwa ndiye chiyembekezo chako? |
|
| 7 |
|
| “Ganiza bwino tsopano: Kodi munthu wosalakwa anawonongekapo nʼkale lonse? Nʼkuti kumene munthu wolungama mtima anaphedwa? |
|
| 8 |
|
| Monga ndaonera ine, anthu amene amatipula zoyipa, ndi iwo amene amadzala mavuto, amakolola zomwezo. |
|
| 9 |
|
| Iwo amaphedwa ndi mpweya wa Mulungu; amawonongeka ndi mpweya waukali wa mkwiyo wake. |
|
| 10 |
|
| Mikango imabangula ndi kulira, komabe mano a mikango yamphamvu amathyoledwa. |
|
| 11 |
|
| Mkango umafa chifukwa chosowa nyama, ndipo ana amkango amamwazikana. |
|
| 12 |
|
| “Mawu anabwera kwa ine mwamseri, makutu anga anamva kunongʼona kwake. |
|
| 13 |
|
| Mʼkati mwa maloto ochititsa mantha usiku, nthawi imene anthu amagona tulo tofa nato, |
|
| 14 |
|
| ndinagwidwa ndi mantha, ndi kuyamba kunjenjemera ndipo mafupa anga onse anaweyeseka. |
|
| 15 |
|
| Pamenepo mzimu unadutsa pamaso panga, ndipo ubweya wa pa thupi langa unayima kuti njoo. |
|
| 16 |
|
| Chinthucho chinayimirira koma sindinathe kuzindikira kuti chinali chiyani. Chinthu chinayima patsogolo panga, kunali zii ndipo ndinamva mawu akuti, |
|
| 17 |
|
| ‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu? Kodi munthu angathe kukhala wangwiro kupambana Mlengi wake? |
|
| 18 |
|
| Ngati Mulungu sakhulupirira atumiki ake omwe, ngati Iye amawapeza angelo ake ndi cholakwa, |
|
| 19 |
|
| nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi, amene maziko awo ndi fumbi, amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche! |
|
| 20 |
|
| Mmawa ali moyo, pofika madzulo afa; mwakachetechete, amawonongeka kwamuyaya. |
|
| 21 |
|
| Kodi zonse zimene ali nazo sizimatheratu, kotero kuti amafa osadziwa nʼkanthu komwe?’ |
|
|
|
|