|
| 1 |
|
| “Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe? |
|
| 2 |
|
| Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake, kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza? |
|
| 3 |
|
| Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo? Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa? |
|
| 4 |
|
| Kodi idzachita nawe mgwirizano kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya? |
|
| 5 |
|
| Kodi udzasewera nayo ngati mbalame, kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo? |
|
| 6 |
|
| Kodi anthu adzayitsatsa malonda? Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse? |
|
| 7 |
|
| Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga, kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba? |
|
| 8 |
|
| Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo, ndipo iweyo sudzabwereranso. |
|
| 9 |
|
| Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza; kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha. |
|
| 10 |
|
| Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa. Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine? |
|
| 11 |
|
| Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere? Zonse za pansi pa thambo ndi zanga. |
|
| 12 |
|
| “Sindidzaleka kuyankhula za ziwalo zake za chirombocho, za mphamvu zake ndiponso za maonekedwe a thupi lake. |
|
| 13 |
|
| Ndani angasende chikopa chake? Ndani angayiyandikire kuti abowole chikopa chake cholimbacho? |
|
| 14 |
|
| Ndani angatsekule kukamwa kwake, pakamwa pamene pazunguliridwa ndi mano ochititsa mantha? |
|
| 15 |
|
| Kumsana kwake kuli mizere ya mamba onga zishango zolumikizanalumikizana; |
|
| 16 |
|
| Mambawo ndi olukanalukana kotero kuti mpweya sungathe kulowa pakati pake. |
|
| 17 |
|
| Ndi olumikizanalumikizana; ndi omatirirana kwambiri kotero kuti sangathe kulekana. |
|
| 18 |
|
| Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali; maso ake amawala ngati kuwala kwa mʼbandakucha. |
|
| 19 |
|
| Mʼkamwa mwake mumatuluka nsakali zamoto ndipo mumathetheka mbaliwali zamoto. |
|
| 20 |
|
| Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi ngati wa mʼnkhali yowira yomwe ili pa moto wa bango. |
|
| 21 |
|
| Mpweya wake umayatsa makala, ndipo malawi amoto amatuluka mʼkamwa mwake. |
|
| 22 |
|
| Mphamvu zake zili mʼkhosi mwake; aliyense wokumana nayo amangoti njenjenje ndi mantha. |
|
| 23 |
|
| Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana ndipo ndi yokhwima kwambiri ndi yolimba. |
|
| 24 |
|
| Pachifuwa pake ndi powuma ngati mwala, ndi pa gwaa, ngati mwala wamphero. |
|
| 25 |
|
| Ngʼonayo ikangovuwuka, ndi anthu amphamvu omwe amaopa; amabwerera mʼmbuyo, kuthawa. |
|
| 26 |
|
| Ngakhale ikanthidwe ndi lupanga, lupangalo silichita kanthu, ngakhale mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera. |
|
| 27 |
|
| Chitsulo imachiyesa ngati phesi chabe ndi mkuwa ngati chikuni chowola. |
|
| 28 |
|
| Muvi sungathe kuyithawitsa, miyala imene ayilasa nayo imangoyinyenyanyenya. |
|
| 29 |
|
| Zibonga zimakhala ngati ziputu; imangoseka pamene akuyibaya ndi nthungo. |
|
| 30 |
|
| Mamba a ku mimba kwake ali ngati chopunthira chakunthwa ndipo imasiya mkukuluzi mʼmatope ngati galeta lopunthira tirigu. |
|
| 31 |
|
| Imagadutsa madzi ozama ngati madzi a mʼnkhali, imachititsa nyanja kuti iwire ngati mbiya yoyengera mafuta. |
|
| 32 |
|
| Kumbuyo kwake imasiya nthubwitubwi zambee, kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi. |
|
| 33 |
|
| Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho, nʼcholengedwa chopanda mantha. |
|
| 34 |
|
| Chimanyoza nyama zina zonse; icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.” |
|
|
|
|