|
| 1 |
|
| Kodi ungathe kuchikoka ndi mbedza ya nsomba chilombo chija cha Leviyatani, kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe? |
|
| 2 |
|
| Kodi ungathe kuchimanga chingwe m'mphuno mwake, kapena kuchiboola nsagwada ndi mbedza? |
|
| 3 |
|
| Kodi chidzakupempha kuti uchimasule? Kodi chidzakupemba kuti uchichitire chifundo? |
|
| 4 |
|
| Kodi chidzachita nawe chipangano kuti chikhale chokutumikira mpaka muyaya? |
|
| 5 |
|
| Kodi ungaseŵere nacho ngati mbalame? Kodi kapena nkuchimanga ndi unyolo kuti adzakazi ako aseŵere nacho? |
|
| 6 |
|
| Kodi asodzi nkuchitsatsa malonda? Nanga amalondawo nkugaŵanagaŵana nyama yake kuti akaigulitse? |
|
| 7 |
|
| Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi ntcheto, kapena kuboola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba? |
|
| 8 |
|
| Ukachiputa, udziŵe kuti pali nkhondo, ndipo iweyo sudzabwereranso. |
|
| 9 |
|
| Ndithu, aliyense akachiwona chilombocho, amataya mtima, ndipo amangodzigwera ndi mantha. |
|
| 10 |
|
| Ngati palibe wina woti angalimbe mtima nkuchiputa. Nanga ndani angalimbe mtima nkukangana ndi Ine Mulungu? |
|
| 11 |
|
| Kodi ndani adandipatsa kanthu, kuti Ineyo ndimbwezere? Zonse za pansi pa thambo ndi zanga. |
|
| 12 |
|
| “Sindingaleke kulankhula za ziwalo zake za chilombocho, za mphamvu zake ngakhalenso za maonekedwe a thupi lake. |
|
| 13 |
|
| Ndani angasende chikopa chake? Ndani angachibaye chikopa chimene chija, kulimba konse kuja ngati chovala chachitsulo? |
|
| 14 |
|
| Ndani angatsekule kukamwa kwake? Mano ake ndi oopsa. |
|
| 15 |
|
| Kumsana kwake kuli mizere ya mamba onga zishango zolumikizanalumikizana, onse olimba ngati mwala. |
|
| 16 |
|
| Mambawo ndi olukanalukana, kotero kuti ndi mpweya womwe sungathe kuloŵa pakati pake. |
|
| 17 |
|
| Ndi olumikizanalumikizana, ndi omamatirana kwambiri, kotero kuti sangathe kutayana. |
|
| 18 |
|
| Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali, maso ake amaŵala ngati kuŵala kwa mbandakucha. |
|
| 19 |
|
| M'kamwa mwake mumatuluka nsakali za moto, mumathetheka mbaliwali za moto. |
|
| 20 |
|
| M'mphuno mwake mumatuluka utsi, ngati wa m'nkhali yogaduka ndiponso ngati wa moto wa mlulu. |
|
| 21 |
|
| Mpweya wake umayatsa makala, malaŵi a moto amatuluka m'kamwa mwake. |
|
| 22 |
|
| Khosi lake ndi lamphamvu kwambiri, aliyense wokumana nacho amangoti njenjenje ndi mantha. |
|
| 23 |
|
| Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana, ndi yokhwima kwambiri, ndipo ndi yolimba. |
|
| 24 |
|
| Pachifuwa pake mpouma ngati mwala. Pali gwa! Ngati mwala wa mphero. |
|
| 25 |
|
| Chilombocho chikangoti vuuku, ndi amphamvu omwe amaopa. Akamva phokoso lake, amachita mantha. |
|
| 26 |
|
| Ngakhale lupanga lichikanthe, silichichita kanthu. Mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera. |
|
| 27 |
|
| Chitsulo chimachiyesa phesi chabe, mkuŵa chimauyesa chikuni choola. |
|
| 28 |
|
| Muvi sungathe kuchithaŵitsa, Miyala imene achilasa nayo, chimangoinyenyanyenya. |
|
| 29 |
|
| Zibonga zimakhala ngati ziputu. Akamachitchaya ndi nthungo, icho chimangoseka. |
|
| 30 |
|
| Za kumimba kwake zili ngati mapale akuthwa. Chimatambalala m'matope ngati galeta lopunthira tirigu. |
|
| 31 |
|
| Chimagadutsa madzi ozama ngati madzi am'nkhali, chimasandutsa nyanja kuti igaduke ngati mbiya yoyengeramo mafuta. |
|
| 32 |
|
| Kumbuyo kwake chimasiya nthubwitubwi zambee, kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi. |
|
| 33 |
|
| Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho, ncholengedwa chopanda mantha. |
|
| 34 |
|
| Chimanyoza nyama zina zonse. Icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.” Mau omaliza a Yobe. |
|
|
|
|